Hazrat Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) Akufuna Kukumana ndi Allah Ta’ala ndi zochita za Hazrat Umar (radhwiyallaahu ‘anhu)

Olemekezeka Abdullah bin Abbaas (radhwiyallaahu ‘anhuma) akunena kuti:

Ndinalipo pa nthawi yomwe mtembo wa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) unkaikidwa pa Jeneza ataphedwa. Anthu anayamba kuthamangira pamene padali thupi lake. Pamene ankayembekezera kuti mtembo wake utulutsidwe ndi kuikidwa m’manda, iwo ankawerenga durood kumfunira zabwino Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndikumamupemphera Umar (radhwiyallahu ‘anhu).

Mwadzidzidzi, ndinapeza munthu kumbuyo kwanga atandigwira paphewa. Nditacheuka kuti ndione amene anali, ndinaona kuti
sadali wina koma olemekezeka Ali (radhwiyallahu anhu).

Pamene ankauyang’ana mtembo wa Hazrat Umar (radhiyallaahu ‘anhu), adati: “E, iwe Umar Allah Taala akuchitire chifundo chapadera!” Kenako adati: “Panthawi ino palibe munthu amene zochita zake zili zokondedwa kwambiri. Ndi zomwe ndikufuna kukumana nazo Allah Ta’ala kuposa zochita zako.” Ndikulumbirira mwa Allah, ndili wotsimikiza kuti Allah Ta’ala akukumanitsa pamodzi ndi anzako awiri, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndi Hazrat Abu. Bakr (radhwiyallahu ‘anhu).

“M’moyo wanu wonse, mudakhalabe ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) komanso Abu Bakr (radhwiyallahu anhu). Choncho, nthawi zambiri ndinkamva Nabi (swallallaahu ‘alayhi wasallam) akunena kuti Ndipita kumalo ena ake ndi Abu Bakr. ndi Umar.Ndidalowa pamalo ena ndi Abu Bakr ndi Umar. Ndidachoka pamalo ena ndi Abu Bakr ndi Umar (Swahiyh Bukhaariy #3685).

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …