Allah ndiye Mlengi ndi Mdyetsi wa zolengedwa zonse. Cholengedwa Chilichonse , ngakhale milalang’amba, dzuŵa, nyenyezi, mapulaneti, kapena nthaka ndi zonse zili m’menemo, ndi zolengedwa za Allah.
Munthu amene amasinkhasinkha ndi kusakasaka za ukulu ndi kukongola kwa zolengedwa zonsezi angalingalire bwino lomwe ukulu ndi kukongola kwa Amene adazilenga!
Allah akutiitanira m’Qur’an Majeed kuti tilingalire ndi kusinkhasinkha za chilengedwe Chake ndipo potero tizindikire ukulu Wake ndi mphamvu Zake. Allah akunena kuti:
إِنَّ فِي خَلْقِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَاخْتِلَافِ اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ لَآيَاتٍ لِّأُولِي الْأَلْبَابِ ﴿١٩٠﴾ الَّذِينَ يَذْكُرُونَ اللَّهَ قِيَامًا وَقُعُودًا وَعَلَىٰ جُنُوبِهِمْ وَيَتَفَكَّرُونَ فِي خَلْقِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ رَبَّنَا مَا خَلَقْتَ هَٰذَا بَاطِلًا سُبْحَانَكَ فَقِنَا عَذَابَ النَّارِ ﴿١٩١﴾
Ndithu, pakulengedwa kwa thambo ndi nthaka, ndikusinthana kwa usiku ndi usana, muli zizindikiro kwa anthu ozindikira. Ndithu, amene amakumbukira Mulungu ali chiimire, ali chikhalire, kapena atagona, ndi kulingalira (poganizira mwakuya) za chilengedwe cha thambo ndi nthaka, (kuti): “Mbuye wathu! Muyeretsedwe, simunagozilenga zonsezi popanda chifukwa, kotero titetezeni ife ku chilango cha Moto wa Jahannam.
Imaam Shaafi’ee Kutsimikizira Kupezeka kwa Allah
Zanenedwa kuti munthu wina osakhulupilira mwa Mulungu adakumana ndi Imaam Shaafi’iy ndipo adamufunsa umboni wokhudzana ndi kupezeka kwa Allah Namalenga.
Imaam Shaafi’e adayankha yekha kuti: “Yang’anani masamba a mtengo wa mabulosi. Mtundu wake, kukoma kwake, kununkhira kwake, kapangidwe kake ndi mawonekedwe a tsamba lililonse n’zofanana.
“Ngakhale kuti ndi wofanana ndendende, madzi ake akamwedwa ndi nyongolotsi ya siliki amasanduka siliki. Njuchi ikadya, uchi umapangidwa. Akadyedwa ndi mbuzi, ndowe zimapangidwa ndipo zikadyedwa ndi mbawala za musk, musk amapangidwa.
“Mapangidwe a mlengi amene ali wamuyaya ndi wamphamvu yonse angapangitse zinthu zambiri zosiyanasiyana kupangidwa kuchokera ku chinthu chimodzi. Kupanda kutero, kulingalira kungafune kuti mapeto a zonse akhale ofanana ndi chinthu chomwe chinalowa m’zinthu zonsezi.”
Imaam Maalik (rahimahullah) Kutsimikizira Kukhalapo/kupezeka kwa Allah Talaa
Munthu wina adadza kwa Imaam Maalik (rahimahullah) n’kumupempha kuti apereke umboni wosonyeza kuti kunja kuno kuli Mlengi.
Imam Maalik (rahimahullah) anayankha nati: “Yang’ana nkhope ya munthu, Ngakhale kuti ndi yaing’ono, nkhope ya munthu aliyense imakhala ndi maso, mphuno, makutu, lilime, masaya, khama, ndi zina.
Ngakhale kuti nkhope iliyonse ili ndi ziwalo zofanana ndendende, palibe nkhope ziwiri zomwe zimafanana ndendende m’maonekedwe ndi mkaumbidwe. Mau ndi osiyana ngakhale milomo ndi yosiyana. “Kusiyana kumeneku komwe munthu aliyense adadalitsidwa nako kungakhale chifukwa cha zotsatira za Namalenga.”
Zizindikiro Zosoyeza Kuti Kuli Namalenga
Munthu wina okhala mchipululu adakalatula ndakatulo iyi:
البعرة تدل على البعير وآثار الأقدام على المسير
فسماء ذات أبراج وأرض ذات فجاج كيف لا تدل على اللطيف الخبير
Pamene ndowe zimasonyeza kuti padutsa ngamira, ndipo mapazi amasonyeza kuti munthu wadutsa.
Ndiye bwanji thambo lodzadza ndi nyenyezi ndi nthaka yokhala ndi njira zodutsamo zisasonyeze kukhalapo kwa Mlengi, Wachifundo chambiri, Odziwa Zonse!
Choncho, munthu akazindikira mphamvu ndi ukulu wa Allah Ta’ala, ayenera kusinkhasinkha ndi kulingalira za chikondi Chake chakuya pa zolengedwa Zake. Ngakhale kuti ndife osamvera ndi osayenera, Iye akupitirizabe kutidalitsa ndi zabwino zosawerengeka, usiku ndi usana.
Allah atidalitse ndi kuthekera kotembenukira kwa Iye ndi kukhala omvera kwa Iye nthawi zonse.