Olemekezeka Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adzikumbutsa za Kuyankha mafunso pa Tsiku Lachiweruzo

Ngakhale Allah Ta’ala adamudalitsa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) pokhala m’gulu la anthu khumi omwe adalonjezedwa kukalowa ku Jannah ali padziko lino lapansi, ndipo ngakhale adali khalifah wachiwiri wa Chisilamu, adali wodzichepetsa kwambiri ndikuwopa kuyankha mafunso pamaso pa Allah Ta’ala pa tsiku la Qiyaamah.

Zikunenedwa kuti nthawi ina, Olemekezeka Umar (radhwiyallahu ‘anhu) adalowa m’munda wina wa zipatso pamodzi ndi Olemekezeka Anas (radhwiyallahu ‘anhu).

Ali m’mundamo Umar radhwiyallahu anhu adapatukira kumbali ndikupita tsidya lina la mundawo ndikumusiya Anas (radhwiyallahu ‘anhu), Sadazindikire kuti Anas (Radhwiyallahu ‘anhu) amamumva kuchokera pomwe adali, ndipo adayamba kudzilankhula ndikudzikumbutsa za kuyankha kwake mafunso pa tsiku lachiweruzo.

Kenako adaziyankhula yekha kuti: “Umar bin Khattaab! Anthu akukuitana ndi dzina loti, Ameer-ul-Mu’mineen! Ngati ukuona kuti ndi chinthu chabwino, Ndikulumbira mwa Allah, iwe mwana wa Khattaab, kumbukira kuti uyenera kumuopa Allah Ta’ala padziko lapansi (pokhala ndi taqwa); apo ayi ndithu Allah adzakulanga pa tsiku la chiweluzo!)” (Muwatta Imaam Maalik #3638)

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …