Chilichonse cha chipembedzo cha Chisilamu chokhudzana ndi akazi chimakhanzikika pa kukhala odzichepetsa komanso wamanyazi. Pachifukwa ichi ndi pamene Chisilamu chikulamula amayi kuti azikhala m’nyumba zawo, kukhala obisika kwa amuna achilendo, komanso kuti asachoke m’nyumba zawo popanda chifukwa chenicheni pa Sharia.
M’mene mkazi walamulidwira kuswali Swalah yake – kuyambira pa chovala chake cha pa Swalah mpaka mumtima mwake pa nthawi ya Swalah – zonsezi zikulozera kuzibisa (thupi lake kwamuna achilendo).
Choncho, kusiya za ibaadah zina zosiyanasiyana za mu Deen, Swalaah ya mkazi yokha ikusonyeza mlingo waukulu waulemu ndi manyazi omwe mkazi amafunikira kusonyeza. Choncho, akulamulidwa kuti atengere ulemu ndi manyazi womwewo womwe amaonetsa mu Swalaah yake asonyezeso chimodzimodzi m’magawo ena a Deeni ndi moyo wapadziko lapansi.
kuzibisa
Ndi mfundo yosatsutsika kuti maonekedwe a akazi ndi osiyana ndi amuna. Shari’ah yazilingalira izi ndipo potero idakhazikitsa ziweruzo zodziwika kwa amuna ndi akazi m’mbali zambiri zofunika za Deen.
Chomwe chimayambitsa zigamulo zodziwika bwino kwa amayi ndikuti adalamulidwa kuchita chilichonse m’njira yobisika kwa iwo. Kusiyanaku kwaganiziridwanso m’maimidwe osiyanasiyana a Swalah. Mkazi akulamulidwa kuti achite kaimidwe kake m’njira yosaonekera komanso yobisika kwambiri.
Imam Baihaqi adanena kuti:
وجماع ما يفارق المرأة فيه الرجل من أحكام الصلاة راجع إلى الستر وهو أنها مأمورة بكل ما كان أستر لها (السنن الكبرى للبيهقي، الرقم: 3196)
Mbali zonse zosiyanasiyana mu Swalaah ya mkazi zomwe zikusiyana ndi Swalaah ya mwamuna (i.e. m’mene amakwaniritsira maimidwe osiyanasiyana a Swalaah) zonse zagona pa satr (kuzibisa).
Mkazi walamulidwa kuchita kaimidwe kalikonse ka Swalaah yake mobisa momwe thupi lake lilili komanso ziwalo zake kwambiri. Sayyiduna Abdullah bin Umar akunena kuti m’nthawi ya Sayyiduna Rasulullah, paswala, amayi ankalangizidwa kuti azizisonkhanitsa ziwalo zawo moyandikana momwe angakwanitsire.