Kusamalitsa komwe olemekezeka Umar (radhwiyallahu ‘anhu)adachita pa kagwiritsidwe ntchito ka chuma cha anthu kunalidi kosasimbika.
Nthawi ina, musk (mtundu wa mafuta onunkhira) anabweretsedwa kuchokera ku Bahrain. Ngati chuma cha anthu onse, Umar (radhwiya allaahu ‘anhu) adati: “Ndikulumbirira kwa Allah! Ndikufuna nditapeza munthu wodziwa kuyeza zinthu kuti andipimire mafutawa kuti ndiwagawe mofanana kwa Asilamu.”
Atamva izi, mkazi wake wolemekezeka Aatikah bint Zaid (radhwiyallahu ‘anha), adadzipereka kuti akwaniritsa ntchito imeneyi nati: “Ine ndiine waluso pakuyeza. Bweretsani ndikuyezereni.” Komabe, Olemekezeka Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adakana.
Kenako mkazi wakeyo adamufunsa chifukwa chomwe adakanira, ndipo iye adayankha nati: “Ndikuopa kuti ukamayeza, ukhoza kutenga mafuta ena amene atsalira pa zala zako ndi kudzipaka Wekha.” Hazrat Umar (radhwiya allaahu ‘anhu) adanenanso kuti: “Ndikuopa kuti ngati ungatikitire manja ako pathupi utapima mafutawa nthawi yolandira gawo lako udzakhala ngati walandira ambiri powerengera ndi omwe unadzipakawo ndipo zidzapangitsa kuti kuti uwapose Asilamu ena onse (ndipo izi sizololedwa)”