Mazhab anayi
Kuyambira nthawi ya Sayyiduna Rasulullah, ma Swahaabah, Taabi’een ndi zaka mazana zotsatira, akazi ankalamulidwa kuswali m’njira yosiyana ndi Swalaah ya amuna m’magawo ena za swalah. Madhabu onse anayi (omwe ndi Hanafi, Maliki, Shafi’i ndi Hambali) onse amagwirizana pa mfundo yakuti Swalaah ya akazi imasiyana ndi Swalaah ya amuna mzochita zina.
khumbo la Sayyiduna Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) pa Akazi Kuswalira Swalah zawo M’nyumba Zawo.
Ngakhale kuti chinali chikhumbo choyaka moto cha Sayyiduna Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) kuti anthu a mu Ummah wake aziswali pamodzi ndi jamaat munzikiti, khumbo la mtima wake linali kuti akazi a mu Ummah wake aziswalira m’nyumba zawo.
Sayyiduna Muhammad (Swallallahu alaihi wasallam) adawalimbikitsa akazi kuti aziswali m’nyumba zawo ndi kukhala obisika kwa amuna (achilendo), kotero kuti adati: “Swala ya mkazi mchipinda chake ndi yabwino kuposa Swalaat yake yomwe akupemphelera pabwalo la nyumba yake, ndipo Swalah yake ya m’kati mwa chipinda chake chogona (kachipinda kakang’ono mkati mwa chipinda chogona) ndiyopambanitsitsa kwambiri kuposa Swalaah yake ya m’chipinda chake chogona.”
Tsiku lina, Sayyidatuna Ummu Humaid, mkazi wa Sayyiduna Abu Humaid As-Saa’idi, adadza kwa Sayyiduna Rasulullah nati: “E, iwe Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam)! Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adayankha: “Ndikudziwa kuti mukulakalaka kuswali pambuyo panga. Komabe, swalah yanu mchipinda chanu ndi yopambana kwambiri kuposa Swalaah yanu m’mbali ina iliyonse ya nyumba yanu. Swalah yomwe ingapempheredwe mbali ina iliyonse ya m’nyumba mwanu ndi yopambana kwambiri kuposa Swalah ya m’bwalo lomwe liri mnyumba. Swalah yomwe yaswalidwa m’bwalo lotsekeredwa mwanu ndi yopindulitsa kwambiri kuposa swalah ya munzikiti wa kwanuko. Swalah ya munzikiti wa kwanuko ndi yopindulitsa kwambiri kuposa Swalaah yako mu Musjid wanga (Musjid Nabawi). Sayyidatuna Ummu Humaid (motsatira ndi kumvera chifuniro cha Sayyiduna Rasulullah), adalamula kuti pakonzedwe malo ang’ono oti aziswalira Swalah yake mkati mwa chipinda chake chogona, ndipo aziswali modzipereka pa malo amenewo mpaka kumapeto kwa moyo wake.