Olemekezeka Aslam (rahimahullah), kapolo wa Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu), akufotokoza kuti Umar (radhwiyallahu ‘anhu) anali ndi mbale zisanu ndi zinayi zomwe zidasungidwa kuti azitumizira mphatso kwa Azwaa-e-Mutwahharaat (akazi olemekezeka a Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) di amayi a Ummah).
Olemekezeka Aslam (rahimahuliah) adanena kuti nthawi iliyonse kukafika chakudya chokoma, zipatso kapena nyama. Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu, ankachigawa magawo asanu ndi anayi pothira m’mbale zisanu ndi zinayi. akatero
ndikutumiza mwaulemu kwa Azwaaj-e-Mutahharat.
Ankatumiza mbale zisanu ndi zitatu zoyambazo kwa Azwaaj-e-Mutahharat ndipo inayo amatumiza momalizira kwa mwana wake okondeka wamkazi amene ndi Bibi Hafsah (radhiyallahu anha)
Nthawi zina, ngati m’mbale ina yake chakudya ndi chochepa, amatumiza mbale iyi kwa mwana wake Bibi Hafsah (radhiyallahu ‘anha), ndikuonetsetsa kuti akazi ena a Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) alandira mbale zonse. Munjira imeneyi Hazrat Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) ankakonda akazi olemekezeka a Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuposa banja lake.