Kudzichepetsa kwa Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu)

Olemekezeka Miswar bin Makhramah (radhwiyallahu ‘anhu) akusimba kuti pamene Umar (radhwiyallahu ‘anhu) anabayidwa, iye anayamba kumva chisoni ndi kukhala ndi nkhawa kwambiri kuudandaulira ummah.

Ibnu Abbaas (radhwiyallahu ‘anhu) adamtonthoza nati: “Oh Ameer-ul-Mu’mineen! Palibe chifukwa chodandaulira. Mudakhala pamodzi ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo mudakwaniritsa ma ufulu ake onse . Ubwenzi wake.” Kenako Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) ndipo mosakhalitsa iye adachoka padziko pano ali osangalatsidwa nanu.

“Kenako mudakhalabe pamodzi ndi Abu Bakr Siddeeq (radhiyallahu ‘anhu) ndipo mudalemekeza ubale umenewu. Hazrat Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu ‘anhu) adachoka padziko lapansi ali okondwera nanu, “Inu mudakhalabe pakati pa Asilamu (ngati mtsogoleri) ndipo mudakwaniritsa maufulu a Ummah. Ngati mutachoka ndi kupatukana nawo, ndithudi, muwasiya ali alokondwera nanu.”

Hazrat Umar (radhiya allaahu ‘anhu) adayankha nati: “Zimene watchulazi zokhudza ubwenzi wanga ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) sizidachitike mukufuna kwanga, zimenezi zidachitika kudzera mu mte3komanso chifundo cha Allah Namalenga zomwe adandipatsa.

“Pankhani ya kukumana kwa Abu Bakr Siddeeq (radhwiyallahu anhu) ndi kundisangalalira kwake, ndiye kuti uwunso ndi ubwino wochokera kumbali ya Allah Ta’ala umene waupereka kwa ine. Potengera ndi m’mene mwandipezera kuti ndikudandaula kwambiri izi ndi chifukwa cha nkhawa imene ndili nayo pa inu komanso Asilamu ena onse a Ummah (kuti zikhala bwanji ndikachoka padziko lapansi pano).

“ Ndikulumbira mwa Allah! Ndikadakhala kuti ndili ndi golide wofanana ndi dziko lapansi, ndikadadzipulumutsa ndekha ku chilango cha Allah Ta’ala ndisanaimirire pa maso pake ndikukumana naye.

Taonani kuopa kwa Sayyiduna Umar (radhiyallahu anhu), ngakhale kuti adapatsidwa nkhani yabwino ya Jannah padziko lapansi ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), uku kunali kulira kwake kumuopa Allah Ta’ala pa nthawi yomwe adali moyo asadamwalire.

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …