Hazrat Umar (radhwiyallahu anhu) Kufuna kuyikidwa pafupi ndi Rasulullah (swallallaahu alaih wasallam)

 

 

 

Pakati pa mphindi zomaliza pambuyo pa Hazrat Umar (radhiliyalahlah ‘Ahu) adaphedwa mwangozi, Anatumiza mwana wake, Hazrat Abdullah Bin Umar (radhwiyallahu ‘Anhuma), kunyumba kwa Hazrat Aaishah (radhiyallahu ‘ahha).

Hazrat Umar (Radhiyallahu anhu adamulangiza iye kuti ukamuuze kuti Umar akupereka Salaam. Usakanene kuti Amiirul muuminiin popeza kuyambira lero sindidzaitanidwanso kuti Amiir-Ul-mu’mineen (chifukwa lero ndimwalira) ukamuuze kuti Umar bin Khattwaab akupempha kuti akaikidwe pafupi ndi abwenzi ake awiri (Mtumiki swallallahu alaih wasallam ndi Abubakr radhwiyallahu anhu).”

Potsatira malangizo abambo ake Abdullah ibn Umar (radhwiyallahu anhuma) adalunjika ku nyumba ya Bibi ‘Aishah (radhwiyallahu anha) komwe adamupeza iye atangokhala kulira ndi kutuluka misonzi pa chipsinjo chimenechi chomwe chigwere Umma kumwalira kwa Umar (radhwiyallahu anhu).

Kutsatira malangizo a abambo ake adapereka salaam. Adanenanso za Salaam ya Umar (radhiyallahu anhu) kwa iye kenako nati,
“Umar akupempha kuti ayikidwe m’manda ndi anzake awiri.” Atamva pempholi, Hazrat Aaishah (radhiyallahu anha) anati, “Ndinkayembekezera kuti ndidzaikidwa m’manda kumeneko (pafupi ndi Rasulullah (swallallaahu alaih wasallam). Komabe, lero ndithandiza Hazrat Umar (radhwiyallahu anhu).” Pamene hazrat abdullah Bin Umar (radhiyallahu ‘Ahuma) adabwerako, ndikunena za Hazrat Umar kuti Hazrat Aaishah (radhiyallah ‘anh) adalola kuti iye aikidwe pamodzi ndi Rasulullah (swallallahu alaih wasallam) ndi Hazrat Abu Bakr (radhwiyallahu anhu).

Hazrat Umar (radhiyallahu anhu) kenako adalangiza mwana wake wamwamuna, Hazrat Abdullah Bin Umar (radhwiyallahu anhuma) akuti, “Ndikapita, mukamanyamula thupi langa, mumupemphenso Bibi Aaishah (radhiyallahu anha) chilolezo kuti Umar akupempha kuti aikidwe limodzi abwenzi ake awiri” Ngati angavomerenso kandiikeni. Ndipo ngati sichoncho mukandiika kumanda
a asilamu ena onse. “ (Saheeh Bukhari # 3700)

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …