binary comment

Swalaah Isanayambe

1. Chisamaliro chapadera chiyenera kutengedwa povala moyenera pa Swalaah. Mkazi ayenera kuvala chovala choterocho chomwe chidzabisa thupi lake lonse ndi tsitsi lake. Ndikusadzipatsa ulemu iye mwini kuvala zovala zothina zomwe zimasonyeza mmene thupi lake lilili kapena kuvala zovala zopyapyala zimene zingachititse kuti ziwalo zenizeni ziwonekere. Ngati chovalacho chili chooneka kuti ziwalo zikuonekera kudzera m’chovalacho, Swalah idzakhala yosavomerezeka.

2. Machenjezo aakulu aperekedwa mu Hadith kwa amayi amene savala moyenerera. Ngakhale chenjezoli likuimira paliponse ndipo silikunena za kuvala mosayenera pa nthawi ya Swalah kokha, munthu angamvetse kuti pamene nkosaloledwa kwa mkazi kuvala chotere kunja kwa Swalaah, ndiye kuti kusaloredwa kuvala zovala zotere akaima pamaso pa Allah mu Swalaah. Kudzakhala kulakwa kwambiri. Kupatula izi, ma Fuqahaa adalemba kuti Swalah ya mkazi yemwe savala bwino pa Swalah komanso amene ziwalo zake zimaonekera kudzera mu chovala chake siiidzakhala chovomerezeka.

3. Phimbani thupi lonse kuphatikizapo tsitsi. Nkhope ndi zikhato zokha zitha kuonekera. Mapazi nawonso aphimbidwe.

4. Ikonzekerenitu Swalah nthawi yake isadakwane.

5. Kupatula kukonzekera kwa thupi (wudhu, ndi zina zotero), muyenera kudzikonzekeretsanso m’maganizo kuti mukukaonekera pa bwalo la Mbuye wanu.

6. Onetsetsani kuti thupi lanu, zovala zanu ndi malo amene mupemphelere ndi za Twahaarah (zoyera).

Check Also

Sajdah

1. Nenani takbira ndikupita pa sajdah. 2. Gwirani manja anu m’mawondo pamene mukupita pa sajdah …