Sayyiduna Umar (Radhiyallahu ‘anhu) Kulamula Zabwino Panthawi Yotsiriza (yamoyo wake)

M’mawa wa tsiku limene Sayyiduna Umar (Radhwiya Allahu ‘anhu) adabayidwa, mnyamata wina adamuyendera nati kwa iye: “Ameer-ul-Mu’mineen! Sangalalani ndi nkhani yabwino yochokera kwa Allah Ta’alal, Inu ndinu Sahaabi wa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) Ndipo inu muli m’gulu la anthu amene adalandira Chisilamu m’masiku oyambirira, ndipo mudasankhidwa kukhala Khalifa ndipo mudachita chilungamo pa utsogoleri wanu wonse, ndipo posachedwapa mumwalira imfa ya Shahiid!”

Atamva izi, Sayyiduna Umar (Radhwiyallaahu ‘anhu) adati: “Ndikusilira kuti zinthu zonsezi (wazitchulazi) ndingasangalare ngati ntchito zanga zonse zabwino zitakhala zongokwanira kuthana ndi zofooka zanga ndikutsala popanda chilichonse chondikomera komanso chotsutsana ndi ine)”.

Mnyamatayu atatembenuka kuti azichoka, Sayyiduna Umar (Radhwiyallahu ‘anhu) adawona kuti chovala chake cha kumusi (buluku) chinali pansi pa timisomali take ndipo chakhudza pansi, Sayyiduna Umar (radhwiyallahu anhu) nthawi yomweyo analamula kuti abwezedwe, ndipo kenako adamuuza. “E, iwe mnyamata! Chikokere chovala Chako mmwamba (ndipo chivale pamwamba pa timisomali tako molingana ndi Sunnah), chifukwa ichi nchoyera pachovala chako komanso ndi njira yomuopa Allah Ta’ala (Bukhari #3700).

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …