1. Yang’anani kuchibula.
2. Sungani mapazi pamodzi kapena pafupi momwe mungakwanitsire. Onetsetsani kuti mapazi ayang’ana kuchibla.
3. Pambuyo pake, pangani Niya ya Swalah yomwe mukuswali ndipo kwezani manja anu mpaka zala zanu zazikulu zigwirizane ndi nsonga zamakutu ndipo nsonga za zala zanu zikhale molingana ndi kumtunda kwa makutu anu.
4. Mukakweza manja m’makutu, onetsetsani kuti zikhato zayang’ana kuchibula ndipo zala zili motalikirana pang’ono.
5. Yambani kunena Takbiir uku mukukweza manja anu ndikumaliza takbeer popinda manja.
6. Pamene mukuwerenga takbeertul ihram (takbeer-e-tahreemah), onetsetsani kuti maso anu ali pa malo a sajdah ndipo mutu wanu watsitsidwa pang’ono.
7. Pindani manja pansi pa chifuwa ndi pamwamba pa mchombo.
8. Gwirani dzanja la kumanzere ndi dzanja lamanja ndi kuika zala za kudzanja lamanja pa mkono wa kumanzere.
9. Yang’anani pa malo a sajdah pamene muli pa Qiyaam.