Pamene Masahaabah (radhiyallahu ‘anhum) adasamukira ku Madinah Munawwarah, madzi omwe adawapeza kumeneko adali ovuta kwa iwo kumwa popeza adali anchere. Komabe, padali Myuda wina yemwe amakhala ku Madinah Munawaarah yemwe adali ndi chitsime chamadzi okoma otchedwa Ruumah, ndipo ankagulitsa madzi a pachitsime chakewo kwa maswahaabah (radhiyallahu ‘anhum).
Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawafunsa ma Swahaabah (radhwiyallahu anhum) kuti: “Ndani amene agule chitsime cha Ruumah kwa Myuda ndikuchipereka kuti chiwathandize Asilamu kuti akhale wolingana ndi Asilamu ena pakutunga madzi ake, ndi kuti Akalandira chitsime ku Jannah posinthanitsa ndi chitsimechi?”
Hazrat Uthmaan (radhwiyallaahu ‘anhu) anapita kwa Myuda yemwe anali mwini wake wa chitsimecho napempha kuti amugulitse madzi a Ruumah. Komabe, Myuda adakana kugulitsa chitsime chonsecho, ndipo m’malo mwake adagulitsa theka la chitsimecho kwa Hazrat “Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) pamtengo wa dirham zikwi khumi ndi ziwiri (12,000).
Sayyiduna ‘Uthmaan (radhwiyallahu anhu) adachipereka chitsimecho nthawi yomweyo kuti Asilamu athandizike. Pambuyo pake ‘ Uthmaan (radhwiya allaahu ‘anhu) adauza Myudayo: “Ngati ukufuna, tipachike zidebe ziwiri pachitsimepa (kuti tonse tidzigwiritsa ntchito chitsimechi nthawi imodzi), kapena ngati ukufuna, nditha kugwiritsa ntchito tsiku limodzi ndipo utha kugwiritsa ntchito tsiku lotsatira.” Myuda adayankha kuti adakonda kusinthana masiku ndi ‘Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) pa kagwiritsidwe ntchito ka chitsimecho.
Pambuyo pake, likakhala tsiku la “Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu), Asilamu ankabwera pachitsimepo ndikutunga madzi okwanira masiku awiri. Ataona kuti Asilamu sakugulanso madzi kwa iye, Myuda uja adati kwa ‘Uthmaan (Radhwiya Allaahu anhu): “Wandionongera chitsime changa (chifukwa sindingathenso kugulitsa madzi kwa anthu! Bwanji osandigula theka linalo.’Uthmaan (Radhwiyallahu anhu) adagula theka lina la chitsimecho popereka ma dirhamu zikwi zisanu ndi zitatu (8000)ndipo adaperekanso kuti Asilamu azithandizika nacho.