10. Mukangoyamba Swalaah, werengani Dua-ul Istiftaah chamuntima:
وَجَّهْتُ وَجْهِيَ لِلَّذِيْ فَطَرَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ حَنِيْفًا مُسْلِمًا وَمَا أَنَا مِنَ الْمُشْرِكِيْنَ إِنَّ صَلَاتِيْ وَنُسُكِيْ وَمَحْيَايَ وَمَمَاتِيْ لله ِرَبِّ الْعَالِمِيْنَ لَا شَرِيْكَ لَهُ وَبِذلِكَ أُمِرْتُ وَأَنَا مِنَ الْمُسْلِمِيْنَ
Ndatembenukira nkhope yanga kwa Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndikukhalabe panjira yoongoka popanda kusokonekera, ndikugonjera kwathunthu, ndipo ine sindine mmodzi wa opembedza mafano. Ndithu, Swalah yanga, nsembe yanga, moyo wanga ndi kufa kwanga ndi za Allah, Mbuye wa zolengedwa. Iye alibe wothandizana naye, ndipo izi ndi zomwe ndalamulidwa, ndipo ine ndine m’modzi mwa ogonjera (Allah).
11. Erengani Ta’awwudh.
Ta’awwudh ndikuwerenga mawu awa:
أَعُوْذُ بِاللهِ مِنَ الشَّيْطَانِ الرَّجِيْم
Ndikudzitchinjiriza kwa Mulungu kuchokera kwa Satana.
12. Kenako yambani qiraat ya Surah Faatihah kenako ndi sura kapena gawo lililonse la Quraan Majeed. Musanayambe kuwerenga surah faathihah, werengani tasmiyah popeza ndi gawo la surah fatihah.
Tasmiyah ndikuwerenga mawu awa:
بِسْمِ اللهِ الرَّحْمٰنِ الرَّحِيْم
M’dzina la Allah, Wachifundo chambiri, Wachisoni.
Dziwani: Azimayi asapemphere mokweza mawu. Swalah iliyonse aziswali mwakachetechete.
13. Lankhulani mawu oti “aameen” pambuyo pa Surah Faatihah.
14. Werengani tasmiyah musadawerenge surah.
Dziwani: Tasmiyah idzawerengedwa (pambuyo pa Surah Faatihah) ngati mungawerenge surah. Ngati wina sayamba Surah iliyonse ndiye kuti tasmiyah isawerengedwe (ngati akuyambira ma Ayah a mkati).
15. Ngati mukuswali rakaah zitatu kapena zinayi, ndiye kuti mu rakaah yachitatu ndi yachinayi mudzawerenga Surah Faatihah yokha basi. Musawerenge sura iliyonse pambuyo powerenga Surah Faatihah.
Dziwani izi: Mu rakaah yachitatu ndi yachinayi ya swala ya fardh, Surah Faatihah idzawerengedwa ndi imaam, muqtadi ndi munfarid (woswali yekha).
Mu Rakaah zonse za sunnah ndi swalah za nafl mudzawerengedwa surah fatihah ndi surah.