Olemekezeka Anas (radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Uthmaan (radhwiyallahu anhu) adanyamuka kupita ku Abyssinia, kusamuka ndi mkazi wake olemekezeka, Bibi Ruqayyah (radhwiyallahu anha), mwana wamkazi wodalitsika wa Rasulullah (swallallaahu alaih wasallam).
Nkhani zokhudza momwe amakhalira zidachedwa, choncho Mtumiki (sallallahu alaih wasallam) adali ndi nkhawa ndipo amatuluka ku Makka Mukarramah kufuna kudziwa za iwo. Pamapeto pake, mkazi wina adadza kwa Mtumiki (sallallahu alaih wasallam ) ndikumuuza za iwo.
Pa nthawiyi, Mtumiki (swallallaahu alaih wasallam) anati: “Hazrat Uthmaan ndi munthu woyamba kuchita Hijrah munjira ya Allah pamodzi ndi banja lake pambuyo pa Nabi Lut.
M’nkhani ina zanenedwa kuti pamene Uthmaan (radhwiyallahu anhu) ankafuna kusamukira ku Abyssinia, Mtumiki (swallallaahu alaih wasallam) adati kwa iye: “Mutenge Ruqayyah pamodzi nawe.
Patapita kanthawi kuchokera pamene anachoka, Mtumiki (swallallah alayhi wasallam) adamufunsa Asmaa mwana wamkazi olemekezeka wa Abu Bakr, kuti awafunse za iwo. Pambuyo pofufuza, adampeza Rasulullah ndi bambo ake olemekezeka Abu Bakr, iye (Asmaa) Adati: “E, Mtumiki (swallallaahu alaih wasallam) wa Allah, ndalandira uthenga kuti Uthmaan tsopano akuyenda kulowera kunyanja ndi banja lake lolemekezeka.
Mtumiki (swallallaahu alaih wasallam) adasangalala ndipo adati: “E, Abu Bakr, iwowo (Uthmaan ndi banja lake) ndi anthu oyamba padziko lapansi kusamuka munjira ya Allah pambuyo pa ma Ambiyaa (Atumiki) awiri, Nabiy Lut ndi Nabiy Ebrahim (alaihimas salaam) omwe adachita Hijrah.”