Ruku ndi I’tidaal

1. Mukamaliza kuwerenga Surah Faatihah ndi surah ina, yimani kaye pang’ono ndipo pambuyo pake kwezani manja (monga momwe tafotokozera mu takbeeratul ihraam) uku mukunena takbira ndikupita pa rukuu.

Zindikirani: Takbeeraat intiqaaliyyah (takbeer yomwe imanenedwa posuntha kuchoka ku kaimidwe kena kupita ku kena) iyenera kuyambika munthu akangoyamba kusuntha kupita ku kaimidwe kena ndipo azingomaliza akafika pa kaimidwe kameneko.

2. Weramani pang’ono mpaka zala zithe kugwira mawondo.

3.  Zikumanitseni zala zanu pamodzi.

Chidziwitso: Munthu sakuyenera kuthinitsa zala zake pamene wagwira m’mawondo kapena kutambasula zala. Momwemonso, mutu ndi nsana sizidzasungidwa moongoka (monga momwe amachitira amuna popanga ruku).

4. Sungani mikono pafupi ndi m’mbali.

5. Timisomali tamapazi onse awiri akhale pamodzi. Ngati izi ndizovuta, ndiye kuti ziyenera kusungidwa moyandikana momwe zingathekere(momwe mungakwanitsire).

Check Also

Sajdah

1. Nenani takbira ndikupita pa sajdah. 2. Gwirani manja anu m’mawondo pamene mukupita pa sajdah …