Sayyiduna Abu Muusa (Radhwiya Allaahu ‘anhu) akufotokoza motere:
Tsiku lina ndidali limodzi ndiMtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) mu umodzi mwa minda ya zipatso zaku Madinah Munawwarah pamene munthu wina adadza napempha chilorezo cholowa m’mundawu, atamva pempho la munthuyo, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) anandiuza. “Mlole alowe ndikumuwuza nkhani yabwino yokhala ndi malo apamwamba ku Jannah (akalowa Jannah ya pamwamba).” Choncho ndinamutsekulira munthuyo ndipo ndinapeza kuti si wina koma Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu). Ndidamufikitsira nkhani yabwino imene Mtumiki (Swallallaahu ‘ alayhi wasallam) adamtchula, ndipo adayamika Allah Ta’ala mothokoza.
Posakhalitsa adadza munthu wina napempha kuti alowe m’munda wa zipatso. Atamva pempho lake, Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa ine: “Mlole alowe ndikumuuza nkhani yabwino yoti akalowa ku Jannah yapamwamba.” Choncho ndinamutsekulira munthuyo, ndipo ndinapeza kuti sanali wina koma Umar (Radhwiyallahu ‘anhu). Ndidamufikitsira nkhani yabwino imene Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamtchula, ndipo adayamika Allah Ta’ala mothokoza.
Patapita nthawi, munthu wina anapemphanso chilolezo choti alowe m’mundamo. Rasulullah (Swallallaahu ´alayhi wasallam) adati kwa ine: “Mlore alowe, ndipo muuze nkhani yabwino yopambana kuti akalowa ku Jannah, limodzi ndi mlandu womwe adzakumane nawo.” Nditatsegula chitseko, ndinapeza kuti munthuyo ali palibe wina koma Uthmaan (Radhwiyallahu ‘anhu). Ndidamuuza zomwe Mtumiki Muhammad (Swallallaahu alaih wasallam) adanena ndipo iye adayamika Allah Ta’ala mothokoza ndipo kenako Adati: “kwa Mulungu yekha ndi komwe timapempha chithandizo.” (Saheeh Bukhari #393)