Ruku ndi I’tidaal

6. Timisomali tamapazi onse awiri akhale pamodzi. Ngati izi ndizovuta, ndiye kuti ziyenera kusungidwa moyandikana momwe zingathekere(momwe mungakwanitsire).

7. Yang’anani malo a sajdah m’maimidwe a ruku (pamene muli pa ruku).

8. Werengani tasbeeh katatu kapena nambala ina iliyonse yosagawika pawiri.

 

سُبْحَانَ رَبِّيَ الْعَظِيْم

Subhaana rabbiyal A’dhwiim
Kuyeretsedwa konse ndi kwa Allah wankulu.

9. weramukani kuchoka pa ruku mukunena ‘tasmee’:

سَمِعَ اللهُ لِمَنْ حَمِدَهْ

\Sami’allahu liman hamidah

Mulungu amamva amene Wamtamanda.

10.  Kwezani manja (monga momwe tafotokozera mu takbeeratul ihraam) ndi kuwaika m’mbali.

11. Nenani tahmeed:

رَبَّنَا لَكَ الْحَمْد

Rabbanaa lakal Hamdu

E, Mbuye wathu, Ndi kwa inu nokha kutamandidwa konse.

Check Also

Sajdah

1. Nenani takbira ndikupita pa sajdah. 2. Gwirani manja anu m’mawondo pamene mukupita pa sajdah …