Kutsatira Njira Yofewa ndi Yodekha Pochita zinthu ndi Anthu:

“Ataa bin Farrookh (rahimahullah) akufotokoza motere:

Tsiku lina lake ‘Uthmaan (radhwiyallaahu ‘anhu) adagula malo kwa munthu wina. Atagula malowa ‘Uthmaan (radhwiyallahu ‘anhu) adadikira kuti munthuyo adzatenge ndalama zake. Komabe, munthuyo sanabwere.

‘Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) adakumana ndi munthuyo pambuyo pake ndipo adamufunsa: “Bwanji sunabwere kudzatenga ndalama zako?” Bamboyo anayankha. “Chomwe chinandipangitsa kuti ndisabwere kudzatenga ndalamazo ndikuti ndidaona kuti simunandigule pa mtengo wake oyenera wamalowa! Aliyense amene ndikumakumana naye akundidzudzula chifukwa chokugulitsa malowa pamtengo otsika” Hazrat Uthman (radhiyallah anhu) adamufunsa kuti: “Kodi ichi ndi chifukwa chenicheni chomwe chakuletsa kubwera kudzatenga ndalama zako?” Adayankha kuti eya bambo uja.

Uthmaan (radhwiyallaahu ‘anhu) adalankhula naye kuti: “Ndikupatsa mwayi wothetsa malonda ndi kukubwezera munda wako, kapena kusiya malonda monga momwe zilili ndi kutenga ndalama zomwe tinagwirizana.

“Uthmaan (radhwiyallaahu ‘anhu) adamufotokozera chifukwa chomwe adamupatsira mwayi wothetsa malondawa kapena kulola kuti apitilize ndikulandira mtengo omwe anagwirizana, iye adati: “Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamupangira duwa munthu wodekha pochita malonda, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Allah Ta’ala amdalitse ndi Jannah munthu amene amakhala ofewa komanso wodekha ndi anthu panthawi yomwe amagula, kugulitsa, kupereka malipiro kapena kupempha malipiro.”

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …