binary comment

Jalsah

1. Nenani takbira ndipo khalani tsonga (jalsah).

2. Phazi lakumanja muliyimike ndi zala zake ndikuyang’anitsa ku qibla. phazi lakumanzere muligoneke ndikulikhalira.

3. Khalani mokumanitsa ntchafu zanu pamodzi (muzikumanitse).

4. Ikani manja anu pa ntchafu ndi zala pamodzi ndipo nsonga za zala zanu zikhale m’mphepete mwa mawondo.

5. Yang’anani malo omwe mukapange sajdah pamene muli chikhalire.

6. Khalani m’malo a jalsah kufikira thupi litakhanzikika ndi ndikudekha musanapite pa sajdah yachiwiri.

7. Werengani dua iyi pa jalsah:

اَلَّهُمَّ اغْفِرْ لِيْ، وَارْحَمْنِيْ، وَعَافِنِيْ، وَاجْبُرْنِيْ، وارْفَعْنِيْ، وَاهْدِنِيْ، وَارْزُقْنِيْ،

Allaahummaghfirlii, warhamni, i wa’aafinii, wajburni,i warfa’ni, wahdinii, warzuqnii.

E, Allah, ndikhululukireni, ndichitireni chifundo, ndifewetsereni, ndichotsereni kufooka kwanga, ndikwezeni pa maso panu, ndipatseni chiongoko ndi kundidalitsa mu zopeza zanga .

8. Nenani takbira ndikupanga sajdah yachiwiri monga mwachizolowezi.

9. Nyamukani kuchokera pa sajdah yachiwiri ndikukhala pansi kwa mphindi zingapo. Kukhala kumeneku kumatchedwa jalsatul istiraahah. Ndi sunnah kuyamba takbira pamene mukunyamuka pa sajdah ndikuitsirizira mukamalizika kuima.

Check Also

Ruku ndi I’tidaal

6. Timisomali tamapazi onse awiri akhale pamodzi. Ngati izi ndizovuta, ndiye kuti ziyenera kusungidwa moyandikana …