Sayyiduna Haani (rahimahullah), kapolo womasulidwa wa Sayyiduna “Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu), akunena kuti: Hazrat ‘Uthmaan (radhiyallahu ‘anhu) ankati akayima pamanda, ankalira kwambiri moti ndevu zake zinkanyowa ndi misozi yake.
Wina adamufunsa kuti: “Timakuwona kuti ukakumbukira Jannah ndi Jahanmum kapena kukambidwa za izo, siumakhudzidwa kwambiri mpaka kuyamba kulira, pomwe ukayima pamanda timakuona kuti umagwidwa ndi mantha kwambiri moti umayamba kulira kwambiri. Chifukwa chiyani?
Hazrat ‘Uthmaan (radhwiya allaahu ‘anhu) adayankha kuti, “Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adati: “Manda ndi gawo loyamba kuchokera kumagawo a tsiku lomaliza. Ngati munthu adutsa malo amenewa ndi kupeza chipulumutso, ndiye kuti pali chiyembekezo chakuti magawo omwe akubwera adzakhala osavuta, ndipo ngati sadutsa malo awa ndi kupeza chipulumutso, ndiye kuti magawo omwe akubwera adzakhala ovuta kwambiri ndi amazunzo kwambiri kwa iye. (Sunan Tirmizi #2308)