Rakaah Yachiwiri

1.Pamene mukudzuka kuchoka pa sajdah, choyamba kwezani chipumi ndi mphuno, kenako zikhato kenako mawondo.

2.Pamene mukuimirira Rakaah yachiwiri, gwirani pansi poika manja anu onse pansipo kuti muthandizikire kunyamuka.

3.Pempherani rakaah yachiwiri monga mwa nthawi zonse (kupatula Dua-ul Istiftaah).

Qadah ndi Salaam

1. Pambuyo pa sajda yachiwiri ya rakaah yachiwiri, khalani tawarruk (kutanthauza kukhala kumanzere ndi kutulutsa phazi lakumanzere pansi pa mwendo wa kumanja). Phazi lakumanja ndi zala zilunjike ku qibla.

Dziwani izi: Kukhala m’malo mwa tawarruk kumagwiranso ntchito pa swalah yomwe ili ndi qa’dah imodzi, mwachitsanzo rakaah ziwiri ndi qa’dah yomaliza ya rakaah inayi. Koma Qa’dah yoyamba ya rakaah zitatu kapena zinayi, wina adzakhala mmalo mwa iftiraash kutanthauza kuti phazi lakumanja lidzakhala choima zala zake zitayang’ana ku qibla pomwe phanzi lamanzere lidzakhala chogona ndikulikhalira.

2. Mukakhala pa tashahhud, tsekani zala zitatu za dzanja lamanja mwachitsanzo chala chapakati ndi zala ziwiri pambali pake. Chala cha shahaadah (chala cholozera) ndi chala chachikulu zidzasiyidwa zotsegula koma chala chachikulu chidzalumikizidwa m’mbali mwa chala cha shahaadah. Ponena za dzanja lamanzere, siyani zala zonse zitatambasulidwa m’mphepete mwa ntchafu. Zala zidzasiyidwa monga mmene zimakhalira ndipo sizidzalumikizana pamodzi.

3. Werengani tashahhud:

اَلتَّحِيَّاتُ الْمُبَارَكَاتُ الصَّلَوَاتُ الطَّيِّبَاتُ لِلّٰهِ السَّلَامُ عَلَيْكَ أَيُّهَا النَّبِيُّ وَرَحْمَةُ اللّٰهِ وَبَرَكَاتُهُ سَلَامٌ عَلَيْنَا وَعَلٰى عِبَادِ اللّٰهِ الصَّالِحِيْنَ أَشْهَدُ أَنْ لَا إِلٰهَ إِلَّا اللهُ وَأَشْهَدُ أَنَّ مُحَمَّدًا رَّسُولُ اللّٰهِ

Attahiyyaatul mubarakaatus swalawaatut twayyibaatu lillah, assalaam alaika ayyuhan Nabiyyu warahmatullah wabarakaatuh, assalaam alainaa wa’alaa ibaadillahis swaalihiin, Ash’hadu anlaa ilaaha illallaah wa ash’hadu anna Muhammadar rasuulullaah.

Ndikupempha kuti ibaadaah zonse zapakamwa zodalitsidwa, ibaadaah zonse zakuthupi ndi ibaadah zonse zokhudza chuma zikhale za Allah yekha. Mtendere wapadera wa Allah utsike pa inu, inu Nabiy, ndi chifundo cha Mulungu ndi madalitso ake (akhale pa inu). Mtendere ukhale pa ife ndi pa akapolo onse oopa Mulungu. Ndikuchitira umboni kuti palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Allah ndipo ndikuikira umboni kuti Sayyiduna Muhammad ndi Mtumiki wa Allah.

4. Pamene mukunena kuti إِلَّا الله, kwezani chala chanu chamkomba phala moloza ku Qibla ndipo chisiyeni choncho mpaka kumapeto kwa qa’dah. Nthawi yokweza chala, yang’anani chala chanu mpaka kumapeto kwa Swalaah.

5. Ngati mukuswali rakaah zitatu kapena zinayi kenako mukamaliza kuwerenga tashahhud m’qa’dah yoyamba, nanunso werengani swalaat alan Nabi (durood). Kenako imirirani Rakaah yachitatu. Musapemphere pambuyo popemphera Swalaat alan Nabi (durood).

6. Pamene mukuimirira Rakaah yachitatu, gwirani pansi poika manja anu onse pa iyo kuti muzithandire kuimilira. Momwemonso mudzalandira chithandizo mukaimirira Rakaah yachinayi.

Check Also

Ruku ndi I’tidaal

6. Timisomali tamapazi onse awiri akhale pamodzi. Ngati izi ndizovuta, ndiye kuti ziyenera kusungidwa moyandikana …