Makhalidwe khumi apadera a Uthmaan (radhwiyallahu anhu)

Hazrat Abu Thawr (rahimahullah) akuti tsiku lina adadza kwa Uthmaan (radhwiyallah”anhu) ndipo adamumva akunena izi panthawi yomwe adaukiridwa. Adati: “Pali ntchito zabwino zokwana khumi zomwe ndadziteteza kwa Allah Taala, ndipo pa ntchito iliyonse ndikuyembekeza kudzalandira malipiro pa tsiku lomaliza;

1) Ndinali munthu wachinayi kuvomereza Chisilamu.

2) Sindinanenepo bodza moyo wanga onse.

3) Sindinayikepo dzanja langa lamanja kumbali yanga yachinsinsi kuyambira nthawi yomwe ndidalonjeza kukhulupirika ndi dzanja langa lamanja kwa Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam).

4) Chiyambireni nthawi yomwe ndimavomereza Chisilamu palibe jumuah imodzi yomwe idadutsa popanda ine kumasula kapolo, ndipo ngati ndilibe kapolo pa Jumaa iliyonse, ndidaonetsetsa kuti ndimumasula kapoloyo pambuyo pake.

5) Sindinachitepo chigololo moyo wanga onse, ndisanavomereze Chisilamu ngakhale nditavomereza Chisilamu.

6)Ndidawakonzekeretsa ankhondo a Tabuuk ndi chuma changa.

7) Ndinadalitsidwa ndi ulemu osonkhanitsa Quraan Majeed mu nthawi ya Mtumiki (swallallaahu ´alayhi wasallam).

8) Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adandikwatitsa mwana wake wamkazi, ndipo atamwalira anandikwatitsanso mwana wake wina.

9) Sindinamwe vinyo m’moyo wanga onse, ngakhale Chisilamu chisanafike kapena pambuyo pa Chisilamu.

10) Ndidali ndi udindo ogula malo ku Madina Munawwarah kuti ndikuuze musjid. zomwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adalonjeza kuti amene waugula adzadalitsidwa ndi Jannah.

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …