Nthawi ina yake Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) analibe chakudya choti adye kotero adavutika ndi njala. ‘Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) atamva kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) akumva njala, nthawi yomweyo mtima wake unadzazidwa ndi nkhawa ndi malingaliro. Chimenecho chinali chikondi chake pa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) kuti sadapume bwino pomwe adadziwa kuti Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adali m’mabvuto ndi mazunzo. Komabe, ‘Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) iye mwini adalibe chakudya chompatsa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam).
Choncho ‘Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) adachoka kunyumba kwake kukasaka ntchito kuti akapeze ndalama yogulira chakudya cha Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam). Kotero ‘Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) anayendayenda kukafunafuna ntchito, atafika pamunda wina wa zipatso wa Myuda wina. ‘Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adadzipereka kuti atungire madzi kuchokera pa chitsimepa ndipo Chidebe chilichonse cha madzi akatunga, Myuda azilipira tende m’modzi.
Myuda adavomera ndipo ‘Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adatungira ndowa khumi ndi zisanu ndi ziwiri (17) zamadzi. Nthawi yolipira itakwana, Myuda adapmupatsa ‘Ali (radhwiyallahu ‘anhu) mwayi okuti atenge mtundu ulionse wa tende omwe ankafuna m’munda wakewu. Choncho, ‘Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adatenga tende khumi musanu ndi muwiri wa mitundu ya ‘Ajwah, kenako adadza naye ndikumupereka kwa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam).
Atapereka tendeyu kwa Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam), Mtumiki (swalla allaahu ‘alayhi wasallam) adalankhula naye ndi pogwiritsa ntchito dzina lake lamtchedzera ndipo adamufunsa: “E, iwe Abul Hasan! wampeza kuti tende uyu?” ‘Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) adayankha kuti: “E, Nabiy wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ndinamva za njala imene mumakumana nayo, choncho ndinapita kukafunafuna ntchito kuti ndikapeze chakudya choti ndikupatseni!”
Atamva izi, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamufunsa kuti: “Kodi wachita izi chifukwa chomukonda Allah Ta’ala ndi Mtumiki Wake (swallallaahu ‘alayhi wa allam)?” ‘Ali (radhwiyallahu ‘anhu) anayankha, “Inde, E, Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)!”
Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Palibe kapolo amene ali ndi chikondi chenicheni pa Allah Ta’ala ndi Mtumiki Wake (swallallaahu ‘alayhi wasallam), kupatula kuti adzayesedwa (nthawi zina) ndi umphawi Choncho, amene ali ndi chikondi chenicheni pa Allah Ta’ala ndi Mtumiki Wake (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ayenera kukhala okonzeka kukumana ndi mayeso a sabr. ”