Allah wadalitsa Ummah wa Sayyiduna Muhammad swallallah alaihi wasallam ndi nyanja yopanda magombe. Nyanja iyi yadzadzidwa ndi ngale, ndi emarodi, ndi marubi, ndi zinthu zina za mtengo wapamwamba pa chuma. Kuchuluka kotenga zinthu mnyanja imeneyi ndiye kuchulukanso kwa phindu lomwe munthuyo angapeze. Nyanja imeneyi siidzatha koma idzapitiriza kumudalitsa munthu chimodzimodzi m’dziko lino ndi lomwe lili mkudza. Nyanja yopanda malire imeneyi ndilo bukhu lolemekekzeka la Qur’an.
Qur’an yolemekezeka ndi mphatso yaikulu ya Allah yomwe adaupatsa Ummah. Ndikulankhula kwa Mulungu kuziyankhula zolengedwa Zake ndipo palibe ubwino pa dziko lapansi umene ungafanane ndi umenewu.
Pomwe Ummah ukuigwiritsitsa mwamphamvu Quraan Majiid ndi kukwaniritsa ma ufulu ake, idzakhala gwero la kuunika kwa iwo m’dziko lino lapansi ndi m’manda. Komanso pa tsiku la Qiyaamah idzatsagana nawo ku zigwa za Qiyamah mpaka kukawalowetsa iwo ku Paradiso.