Kulimba Mtima kwa olemekezeka Ali (radhiyallahu ‘anhu)

Pa nkhondo ya Uhud, Sayyiduna Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adawonetsa kulimba mtima kwambiri polimbana ndi adaniwo. Choncho, iye yekha ndiye anali ndi udindo opha atsogoleri anayi a chiQuraishi, omwe mwa iwo anali Talhah bin Abi Talhah.

Nkhondo itatha, adapereka lupanga lake kwa mkazi wake olemekezeka, Bibi Faatimah (radhwiyallahu ‘anha), kuti atsuke magazi, ndipo adabwereza mau awa:

أفاطم هاك السيف غير ذميم     فلست برعديد ولا بلئيم

لعمري لقد أبليت في نصر أحمد     ومرضاة رب بالعباد عليم

Iwe Fatimah! Tenga lupanga ili, pamene oligwirayo alibe mlandu uliwonse, pakuti sindinali wamantha (pankhondoyo), ndiponso sindidachite zinthu ngati munthu wachabe ndi oipitsitsa (ndiye kuti, Ndidamenya nkhondo m’nkhondo yolondola ndikuwonetsa kulimba mtima kotheratu).

Ndi moyo wanga. Ndidapereka mphamvu zanga zonse pothandiza Ahmed (mtendere ukhale pa iye), ndi kupeza chiyanjo cha Mbuye wanga yemwe ali ndi kudziwa konse zokhudza akapolo Ake.

Atamva izi, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) nthawi yomweyo adachitira umboni zomwe adanenazo. Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adanena kwa iye. “E, iwe Ali, wamenya bwino, ndipo Aasim bun Thaabit, Sahl bun Hunaif, Haarith bun Simmah ndi Abu Dujaanah nawonso wamenyana bwino.” (Majma’uz Zawa’id #10116-10118, Mustadrak Hakim #4310, Makarim-ul-Akhlaq #195)

Check Also

Mantha a Olemekezeka Talha (radhwiyallahu annhu) kuopa kuti Chuma cha Padziko Lapansi chisamuchititse Osakumbukira Allah Ta’ala.

Nthawi ina, Olemekezeka Talha (radhwiyallahu anhu) adalandira ndalama zokwana ma dirham zikwi mazana asanu ndi …