Mnyumba momwe Mukuwerengedwa Qur’an

M’ Hadith yolemekezeka, zatchulidwa kuti nyumba yomwe mumawerengedwa Qur’an Majiid imakhala ndi madalitso, kotero. Angelo amaunjikana mmenemo komanso chifundo cha Mulungu chimatsikira m’menemo.

Zidanenedwa zokhudza nkhani ya olemekezeka Ubaadah Ibn Saamit (radhwiyallahu anhu) kuti “Nyumba yomwe imawerengedwa Qur’an ndenga lake limakutiridwa ndi Nuru imene angelo akumwamba amafunafuna chiongoko ndi kuwala monga m’mene ngalawa imayendera pakati nyanja kapena oyenda pa nthaka kufuna njira ndi kuunika kudzera mu nyenyezi yonyezimira.”

Mu Hadith ina zikunenedwa kuti nyumba yomwe Quraan Majiid imawerengedwa, kuwerengako kumalowetsa madalitso m’banja, ndikuwatsitsira angelo pa iwo komanso imathamangitsa ma shayaatiin panyumba, ndikupangitsa ubwino kuchulukirachulukira m’nyumba, koma m’nyumba yomwe Qur’an Majiid mulibe Siimawerengedwa, Ndi kuti moyo m’menemo Umakhala wokhazikika, Angelo kusiya nyumbayo ndipo shayaatiin amakhalamo, nyumba yoteroyo ilibe ubwino.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …