Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamuika Sayyiduna Ali (radhwiyallahu ‘anhu) kutsala ku Madina Munawwarah

Pa nthawi ya Nkhondo ya Tabuuk, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) pochoka ku Madinah Munawwarah, adamusankha Ali (radhiyallahu ‘anhu) kuti aziyang’anira ntchito za m’ Madina Munawwarah pakakhala kuti iye kulibe.

Choncho, ndi malangizo a Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam), Ali (radhwiyallahu ‘anhu) sadatuluke ndi gulu lankhondo, koma adakhalabe ku Madina Munawwarah.

Pambuyo pake, anthu ena anayamba kufalitsa mphekesera yoti chifukwa chimene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamuuzira Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) kuti atsale ndi chakuti iye waipidwa naye. Atamva izi, Ali (radhwiyallahu anhu) nthawi yomweyo adadza kwa Mtumiki (swallallaahu ‘alaihi wasallam) namufotokozera zomwe anthu ena anali kunena.

Malinga ndi ma Hadith ena, Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adanena kwa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam).
wasallam, “E, Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Ine sindikufuna kuti ma Arabu ena aziyankhula za ine kuti; “ Mtumiki wa Allah wamusiya nsuweni wake (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam)) ndipo watsalira.” Komanso chinali chikhumbokhumbo chachikulu cha Ali (radhwiyallahu anhu) kuti alowe usilikali kuti akathe kumenya nkhondo munjira ya Allah Ta’alaa. Malinga ndi ma Hadith ena, Ali (radhwiyallahu ‘anhu)
Adati kwa Mtumiki (swallallaahu ‘alaih wasallam): “E, Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Kodi mukundisiya pamodzi ndi akazi ndi ana?” Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamtonthoza nati kwa iye: “Kodi iwe sukusangalala Kukhala ndi ine kudzakhala monga momwe Haruun analili ndi Muusa (alaihimas salaam), kupatula kuti palibe Nabiy amene adzanditsatira pambuyo panga?” M’mawu ena, pamene Nabii Musa (‘alaihis salaam) anapita ku phiri la Tuur, anamusiya mchimwene wake Nabi Haruun (‘ alaihimus salaam), kuyang’anira anthu. Izi zidasonyeza udindo wapamwamba wa Nabi Haruun (‘alaihis salaam) komanso kudalira komwe Nabii Musa (‘ alaihis salaam) anali nako pa iye.

Momwemonso, Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamudziwitsa Ali (radhwiyallahu ‘anhu) kuti kumuika kukhala woyang’anira ntchito za Madina Munawwarah iye kulibe ndi chizindikiro chakuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ali ndi chiyembekezo pa iye.

Hazrat Ali (radhwiyallaahu ‘anhu) atamva izi nthawi yomweyo adati: “Ndasangalala, ndasangalala (ndi ganizo la Allah Ta’ala ndi Mtumiki Wake (swallallaahu ‘alayhi wasallam)).

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …