M’hadith inayake, zanenedwa kuti nthawi zonse munthu amene waphunzira Qur’an Majeed (kapena gawo lina lake) akaimirira kuswali gawo lina la usiku kuti aiwerenge, ndiye kuti usiku umenewu umadziwitsa usiku wotsatira za izi zapadera. mphindi zomwe zinali zosangalatsa. Usiku umalimbikitsa usiku otsatira kuti udikire mwachidwi nthawi zapadera zomwe munthu ameneyu adzayimilire kuti awerenge Qur’an pa Swalaah. Usiku umapemphanso kuti usiku wotsatira ukhale wosangalatsa kwa iye.
Madalitso a Qur’an kuyendelera pamene Munthu wamwalira
Monga momwe madalitso a Quraan yolemekezeka amasangalatsa pa dziko lapansi, momwemonso madalitso a Quraan Majiid amapitiriza kuyenderera ku moyo otsatira. Qur’an Majeed imamthandiza munthu m’manda ngakhale pa Tsiku Lomaliza, mpaka kukam’lowetsa ku Paradiso. M’nkhani ina idanenedwa kuti, munthu amene adali odzipereka pa Qur’an Majiid m’moyo wake, akamwalira, ndiye kuti denga la Nuur yomwe inkafungatira nyumba yake nthawi ya moyo wake, limachotsedwa pansi ndikunyamulidwa. Choncho angelo amayang’ana ali kumwamba koma sakuona kuwalako. “Pambuyo pa imfa yake, pamene moyo wake ukudutsa m’mitambo (kukakumana ndi Allah), angelo a ntambo ulionse amakumana naye, ndipo kuchokera mu mizimu yonse, amakondwera naye ndi kumupemphera iye mapemphero apadera. Kenako amakumana ndi angelo amene akhala naye nthawi yonse ya moyo wake akumuteteza ku zoipa, ndipo iwo pamodzi ndi angelo ena amampemphera chikhululuko mpaka tsiku la Qiyaamah.
[1] ورواه ابن أبي الدنيا وغيره عن عبادة بن الصامت موقوفا عليه ولعله أشبه كذا في الترغيب والترهيب للمنذري 1/ 245
[2] ورواه ابن أبي الدنيا وغيره عن عبادة بن الصامت موقوفا عليه ولعله أشبه كذا في الترغيب والترهيب للمنذري 1/ 245