Kumail bin Ziyaad (rahimahullah) akuti:
Nthawi ina ndinatsagana ndi Ali (radhwiyallahu ‘anhu) pamene ankatuluka mumzinda wa Kufah ndikupita ku Jabbaan (kumapeto kwa mzinda wa Kufah). Atafika ku Jabbaan, Ali (Radhwiyallahu ‘anhu) anatembenukira kumanda ndikufuula. “E inu anthu okhala m’manda! E, inu anthu amene matupi awo anavunda! E inu anthu osungulumwa! Kodi muli bwanji? Momwe ife (padziko lapansi pano) tiliri ndi kuti chuma cha anthu anamwalira chasakazidwa ndikugawidwa, ana aakazi a anthu akufa ndi amasiye ndipo akazi a omwalirayo akwatiwanso. Umu ndi momwe tilili. Choncho tidziwitseni za chikhalidwe chanu (m’manda)?”
Kenako Ali (radhwiya Allaahu ‘anhu) adatembenukira kwa ine nati: “E iwe Kumail! Ngati anthu a m’mandawa atawalola Allah Taala kuyankha kuitana kwathu, akanati: “Zotsatira zabwino (za tsiku lomaliza). ndiko kukhala ndi taqwa.”
Kenako Ali (radhwiya allahu ‘anhu) anayamba kulira nati: “E, iwe Kumail! Manda, ndithudi, ndi bokosi lomwe muli zochita za munthu. Ndi nthawi ya imfa yokha yomwe munthu adzadziwe ntchito zake zomwe adatsogoza zikumudikirira m’manda mwake (komwe ndi momwe munthu adzakhalite m’manda kulangidwa kapena kusangalala zidzatsimikizira za momwe akakhalire umoyo umene uli nkudza)