Kulimba Mtima kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu) pa Nkhondo ya Khaibar

Pa nkhondo ya Khaibar, Mtumiki (swallallahu ‘alaihi wasallam) atapereka mbendera ya Chisilamu kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu), Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adatsogolera gulu lankhondo. Maswahaaba ku bwalo la Qamoos.

Atayandikira bwalolo, msilikali wina wachiyuda, dzina lake Marhab, anatuluka kudzamenyana nawo. Marhab anali msilikali otchuka amene anali wodziwika ndi mphamvu zake zambiri ndi kulimba mtima kwake. Choncho, Marhab pamene adakumana ndi Ali (radhwiyallahu anhu) ndi Asilamu, adayamba kudzitamandira chifukwa cha kulimba mtima kwake pankhondo polakatula mau awa:

قَدْ عَلِمَتْ خَيْبَرُ أَنِّيْ مَرْحَبُ

Anthu aku Khaibar onse akudziwa bwino kuti ndine Marhab

شَاكِيْ السِّلَاحِ بَطَلٌ مُجَرَّبُ

Ndine msilikali odziwa zida za nkhondo komanso odziwa kumenya nkhondo

إِذَا الْحُرُوْبُ أَقْبَلَتْ تَلَهَّبُ

(Onetsani mphamvu zanga zenizeni ndi kulimba mtima kwanga) panthawi yomwe nkhondo ikuyamba ndipo nkhondoyo ikuyaka ndikukulirakulira.

Atalankhula mawu amenewa iye adawachalenja Asilamu kuti abwere kudzamenyana naye. Poyankha tchalenji yake, Aamir bin Akwa (radhwiyallahu anhu) adatuluka. Aamir (radhwiyallahu anhu) adakumana ndi Marhab ndipo adalakatula mawu awa:

قَدْ عَلِمَتْ خَيْبَرُ أَنِّيْ عَامِرُ

Anthu aku Khaibar amadziwa bwino kuti ndine Aamir

شَاكِيْ السِّلَاحِ بَطَلٌ مُغَامِرُ

Kuti ndine wankhondo yemwe ali ndi zida zonse ndipo ali okonzeka kulowa nawo munkhondo iliyonse.

Nkhondoyo idayamba pomwe Marhab adamenya koyamba. Adazunguza lupanga lake m’mwamba pafupi ndi ‘Aamir (radhwiyallahu anhu) yemwe adalibolka ndi chishango chake cholimba. Kumenyetsa kwa lupanga la Marhab kunali kwamphamvu kwambiri kotero kuti kumenya chishangocho, kudadinda pa chashangocho, Aamir (radhwiyallahu anhu) adapezerapo mwayi kuti amenye Marhab koma adamuphonya ndipo lupangalo lidamubwelera mwini ndikuvulala modetsa nkhawa.

Kenaka Ali (radhwiyallahu anhu) adalowa ndikumutchalenja Marhab, Marhab adzabwerezanso ndakatulo yake ija ponena kuti:

أَنَا الَّذِيْ سَمَّتْنِيْ أُمِّيْ حَيْدَرَهْ

Ndine amene amayi ake anamutcha kuti Haydar (Mkango Wolusa)

كَلَيْثِ غَابَاتٍ كَرِيْهِ الْمَنْظَرَهْ

Monga mkango owoneka owopsa wa m’nkhalango

أُوْفِيْهِمْ بِالصَّاعِ كَيْلَ السَّنْدَرَهْ

Ndikafuna kusinthana ndimapereka mulingo okwanira (ndiye kuti kumenya kwanga ndi mapeto, ndipo ndimapha adani Mwamsanga.)

Pankhani ya Ali (radhwiyallahu ‘anhu) kudzitchula kuti Haydar (mkango olusa), zikunenedwa kuti pamene Ali (radhwiyallahu ‘anhu) ankabadwa, bambo ake Abu Taalib adali atapita paulendo ndipo kunalibe ku Makkah Mukarramah. Choncho, amayi ake anamutcha kuti Haydar (kutanthauza mkango). Anamucha dzina la abambo ake Hadar omwe dzina lawo linali Asadi (kutanthauza kuti mkango). Abu Taalib atabwerera ku Makka Mukarramah kuchokera ku ulendo wake ndipo mkazi wake adamuuza kuti wamutcha mwana wawo Haydar, adasintha dzina la mwana wake ndikumutcha dzina loti “Ali, iyeyu adatchuka ndi dzina limeneli lomwe adapatsidwa ndi bambo ake komabe pa nthawiyi adadzitchura yekha dzina lomwe adapatsidwa ndi mayi ake.

Mbiri ina imanena kuti Marhab analota maloto usiku oti mawa ndi nkhondo ndipo anaona kuti mkango unakhadzuridwa pakati. “Allaamah Zurqaani (rahimahullah) wanena kuti Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adadalitsidwa ndi chidziwitso cha izi kudzera mu kasht (kuuzidwa m’maganizo, kudzera m’maloto kapena njira ina). Ndichifukwa chake adadzitchula yekha pogwiritsa ntchito dzinali. “Haydar, kutanthauza kuti mkango olusa, mu ndakatulo yake. Podzitcha kuti iye ndi mkango olusa, Marhab adazindikira kuti maloto ake anawonetsa kuti akumana ndi mapeto moyo wake kudzela mu lupanga la Ali (radhwiyallahu ‘anhu). Zimenezi zidamuchitsa iye kukhala mantha komanso kusweka mtima.

Kenako adayamba kumenyana, ndipo ndi kamodzi komwe adamenyako Ali (radhwiyallahu anhu) adaswa mutu wa Marhab, katswiri otchuka wa nkhondo ya Khaibar, nachotsa moyo wake. Kenako Allah Ta’ala adadalitsa Ali (radhwiyallahu Anhu) pogonjetsa balo limeneli. (Saheeh Bukhaari #4210, Saheeh Muslim #1807, Majma’uz Zawaa’id #10206, Fat-hul Baari 7/535-549, Sharun Nawawi vol. 12 pg. 185 and Sharhuz Zurqaani 3/244-258)

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …