Kuonjezera apo, zikunenedwa kuti akamwalira munthu amene waigwira mwamphamvu Quran Majiid, kenako asanaikidwe, banja lake likadali pamaliro ake, Qur’an Majiid imadza kwa iye ili ndi maonekedwe okongola ndikuyimirira pafupi ndi iye. kumutu, kumuteteza ndi kumtonthoza mpaka atakulungidwa mu kafani (sanda). Kenako Quraan Majiid imalowa munsaluyo ndikugona pachifuwa chake.
Akaikidwa m’manda, n’kuikidwa nthaka pamwamba pake, ndipo anzake onse atachoka, kenako angelo, Munkar ndi Nakiir, amadza kwa iye ndikukhala limodzi m’manda mwake. Kenako Quran imadza pakati pake ndi Angelo.
Angero amalankhula k uiwuza Quraan Majiid kuti: “Choka kuti timufunse mafunso.” Koma Quraan Majiid imayankha kuti: “Sindichokapo! ” inu gwirani ntchito iliyonse (yomufunsa), koma ndisiyeni ndikhale naye pano, ndikulumbilira mwa Allah iyeyu anali bwenzi langa nthawi zonse ndiye sindingamusiye mpaka nditakamulowetsa ku Jannah.”