Tsiku lina, m’nthawi ya Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) gulu la maswahaaba a fuko la Banu Al-Ash’ar lidayenda kuchokera ku Yemen kupita ku Madina Munawwarah ndi cholinga chopanga hijrah.
Atafika ku mzinda odalitsika wa Madinah Munawwarah, adapeza kuti chakudya chawo chomwe adabwera nacho chatha. Choncho adaganiza zotumiza mmodzi mwa maswahaba awo kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kuti akamupemphe kuti awakonzereko chakudya.
Koma Mnzawoyo atafika pakhomo la nyumba yodalitsika ya Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adamumva Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) akuwerenga mobwerezabwereza ndime iyi ya Quraan Majiid:
وَمَا مِن دَابَّةٍ فِي الْأَرْضِ إِلَّا عَلَى اللَّهِ رِزْقُهَا وَيَعْلَمُ مُسْتَقَرَّهَا وَمُسْتَوْدَعَهَا ۚ كُلٌّ فِي كِتَابٍ مُّبِينٍ ﴿٦﴾
Palibe cholengedwa chilichonse padziko lapansi chimene riziki lake silimaperekedwa ndi Allah. Amadziwa malo ake okhalitsa ndi akanthawi kochepa. Chilichonse chili (chinalembedwa) m’Buku lomveka bwino.
Atamva ndime iyi ya Qur’an Majiid, Mnzawoyo adadzifunsa yekha kuti: “N’chofunika kwanji kuti tipereke pempho lathu kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) pamene Allah mwini watenga udindo wopereka riziki kwa zolengedwa zonse?”
Adati mumtima mwake: “Ife anthu a Banu As-Ash’ar, siife onyozeka poyerekeza ndi nyama pamaso pa Allah. Choncho, Allah Ta’aala, Wachifundo Chambiri ndi Wachisoni atipatsa riziki.”
Ndi ganizo ili m’maganizo mwake, sadapereke pempho la anthu ake kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam), M’malo mwake, nthawi yomweyo anachoka pakhomo n’kubwerera kwa anthu ake.
Atabwerera kwa anthu ake adawayankhula nati: “E, inu abwenzi anga! Maswahaaba ake a Ash’ari anazindikira kuti mawu akewo akutanthauza kuti iye adaufikitsa uthenga wawo kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ndi kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) awakonzera chakudya posachedwa.
Kenako, adawona amuna awiri akubwera kwa iwo, atanyamula thireyi yayikulu yodzaza ndi nyama ndi mkate. Anthu awiri aja anapereka chakudya chonse kwa iwo n’kunyamuka. Kenako maswahaaba a Ash’ari adakhala pansi ndikusangalala ndi chakudyacho, nadya mpaka kukhuta.
Atamaliza kudya adapeza kuti m’thireyi munatsala chakudya chokwanira, ndipo adaganiza kuti n’koyenera kukabweza chakudya chotsalacho kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kuti akachigwiritse ntchito momwe angafunire. Choncho adalamula awiri mwa maswahaaba awo kuti akapereke chakudyacho kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam).
Pambuyo pake, onse atakaonekera kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam), adamuthokoza chifukwa cha chakudyacho ndipo adamuuza kuti sanalawepo chakudya chokoma ngati chomwe adawatumiziracho. Atamva izi, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) anadabwa kwambiri ndipo adati kwa iwo: “Sindidakutumizireni chakudya.”
Kenako adamufotokozera Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kuti iwo anamtuma mmodzi mwa maswahaaba awo kuti akamupemphe chakudya choti adye, ndipo atabwerera adawauza nkhani yabwino yoti thandizo la Allah liwapera posachedwa. Izi zidawapangitsa kukhulupirira kuti chakudya chomwe adalandira chidatumizidwa ndi Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) mwini wake.
Kenako Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adawaitana Swahaabah wachi Ash’ari yemwe adamutuma uja ndipo adamufunsa chifukwa chomwe sadamufotokozere Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) zomwe anzakewo anamutuma. Kenako adamufotokozera Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) zomwe zidachitika.
Atamva nkhani yonse, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adawauza kuti chakudya chomwe adalandira sichidatumizidwe ndi iye, anatumiza kwa iwo ndi Allah, Yemwe watenga udindo opereka chakudya kwa zolengedwa zonse.