Olemekezeka Ali (radhwiyallahu ‘anhu) akusimba kuti nthawi ina, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adapita ku maliro a Swahaabah wina wake. Kenako adalankhula ndi ma swahaabah (radhiyallahu ‘anhum) omwe adalipo Ndipo adati: “Ndani mwa inu adzabwerera ku Madinah Munawwarah, ndipo paliponse akakawona fano kapena chiboliboli adzaziphwanya, ndipo paliponse pamene akaone mtumbira wa manda wautali (okwera kwambiri mwamba, kapena omangidwapo adzazilinganiza (pa utali woyenerera), ndipo paliponse pamene angakaone chithunzi (cha zinthu zamoyo), akaononga nthawi yomweyo?”
Sahaabi wina atamva izi adadzipereka nati: “Nditero oh Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)!”
Koma asadalowe mumzindawo, adagwidwa ndi mantha a anthu ake, ndipo adabwerera kwa Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) nasonyeza kulephera kwake kukwaniritsa ntchito yotere. Ali (radhwiyallahu ‘anhu) anali pomwepo ndipo adati kwa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wa allam), “Ndipita oh Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasalam)!”
Ali (radhwiyallahu ‘anhu) adapita ku Madinah Munawwarah namaliza ntchito yomwe adapatsidwa.
Pobwerera, adati kwa Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam), “E inu Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)! Sindinasiye m’mudzi fano ngakhale chiboliboli kupatula kuti ndaphwanya, kapena mtumbira omwe unakwera pamwamba ndipo waikidwa pa mlingo wake oyenera), kapena chithunzi chilichonse (cha zinthu zamoyo); kupatula kuti ndachiononga.”
Pambuyo pake Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Amene abwerera kudzachita chimodzi mwa zinthuzi (ndikukweza mitumbira pamwamba pa utali wolondola kapena zomanga pamwamba pawo, kapena kupanga zithunzi zamoyo, kenako wasonyeza kusalabadira ndi kusayamikira zomwe zidavumbulutsidwa kwa Muhammad (swallallaahu ‘alayhi wasallam) (i.e. wasonyeza kusalemekeza malamulo a dini amene adavumbulutsidwa kwa Mtumiki (sallallahu ‘alayhi wasallam))”
Kuchokera mnkhaniyi, tikuwona kulimba mtima kwapadera kwa Ali (radhwiyallahu ‘anhu), pamodzi ndi kufunitsitsa kwake kukwaniritsa nthawi zonse lamulo lodalitsika la Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam).