Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid

1. Onetsetsani kuti mkamwa mwanu ndimoyera musanambe kuwerenga Qur’an Majiid.

Kwanenedwa kuti Ali (radhwiyallahu anhu) adati: “Ndithu, pakamwa panu ndi njira ya Qur’an Majiid (pakamwa panu mumawerenga Qur’an Majiid). Pa chifukwa chimenechi, tsukani mkamwa mwanu pogwiritsa ntchito miswaak.

2. Inyamureni Quraan Majiid Mwaulemu kwambiri ndipo nthawi zonse iyikeni pamalo Olemekezeka mwaulemu. Musaike Quraan Majiid pansi kapena pamalo aliwonse pomwe siidzalemekezedwa.

3. Musaike chilichonse pamwamba pa Quraan Majiid, ngakhale chitakhala chitaab chokamba za Dini.

4.Nkosaloredwa kugwira Quraan Majiid popanda wudhu.

Abdullah bin Umar (radhwiyallahu anhuma) akusimba kuti Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ndi munthu yekhayo amene ali mu wudhu amene angakhudze Qur’an.

5. Pa nthawi yowerenga Qur’an Majiid, zili Mustahab kwa munthu kukhala ndi wudhu, kuvala zovala zoyera (zatwahaarah ndi kuyang’ana pachibla. Koma ngati munthu asayang’ane ku Qiblah kapena alibe wudhu uku akuwerenga Quraan Majiid, nzoloredwa (ngati sakhudza Quraan Majiid).

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …