Du’aa yapadera ya Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam)

Olemekezeka ‘Aaishah bint Sa’d (radhwiyallahu ‘anha), mwana wamkazi wa olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu), akufotokoza motere kuchokera kwa abambo ake, Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu):

Pa nkhondo ya Uhud. (Pamene adani adaukira kumbuyo kwawo ndipo ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) ambiri adaphedwa pabwalo lankhondo), ma Swahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) sadathe kumpeza Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ndipo ankaye ndayenda mozunguzika. Pa nthawiyo ndinasunthira pambali ndikudziuza ndekha kuti, “Ndipitiriza kumenyana ndi makafiri. Pamene ndikumenya nkhondoyo, ndikhoza kuphedwa kapena Allah Ta’ala andilole kuti ndikhalebe ndi moyo. Ngati ndipulumuke pankhondoyi. Ndithu, ndikumana ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam).

Ndili mkatikati moganiza zimenezi, ndinangoona munthu akuphimba nkhope yake zomwe zidapangitsa kuti ndisamuzindikire. Osakhulupirira adayandikira kwa iye mpaka ndidadziwuza ndekha kuti: “Amulondola mpaka amupeza.” Nthawi yomweyo munthuyo adadzadzitsa m’manja mwake miyala ndi kuiponya pa nkhope za osakhulupirirawo, ndipo iwo adatembenukira zidendene zawo ndikubwerera mpaka kukafika kuphiri. Munthuyo anabwereza zimenezi kangapo (pamene osakhulupirira ankafuna kumuukira), ndipo sindinadziwe kuti anali ndani (popeza nkhope yake sindinkaiona).

Pakati pa ine ndi munthu uyu panali Miqdaad bun Aswad (radhwiyallahu ‘anhu). Ndinangoganiza zomufunsa Miqdaad (radhwiyallahu ‘anhu) kuti munthu olemekezekayu anali ndani? Miqdaad (radhwiyallahu ‘anhu) Adandiuza: “E, iwe Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu)! Ameneyo ndi Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) amene akukuitana!” Ndidamufunsa Miqdaad (radhwiyallahu ‘anhu): “Ali kuti Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam)?” Poyankha Miqdaad (radhwiyallahu ‘anhu) adalankhula ndi munthu yemweyo.

Pozindikira kuti munthuyu sanali wina koma Mtumiki okondedwa wa Allah Ta’ala (swallallaahu ‘alayhi wa wasallam), nthawi yomweyo ndinayimilira m’malo mwanga, ndipo chifukwa cha chisangalalo chadzaoneni, ndidakhala osalabadira za mabala anga. Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati kwa ine: “E, iwe Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu)! Unali kuti nthawi yonseyi?” Ndidayankha nati: “Ndidali nditaimirira patali ndi inu, pomwe ndimakuonani (kufikira adani adakuukirani ndikukutayani).

Kenako Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adandikhazika patsogolo pake ndipo ndidayamba kuponya mivi kwa makafiri uku ndikuwauza: “E, Allah! Uyu ndi muvi wanu; Pamene ndimaponya miviyo, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankandipemphera duaa kuti: “E, Allah! Yankhani du’aa la Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu)! E, Allah! Ipangeni mivi ya Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) kulungama kwa adani!” Kenako Rasulullah (swalla allaahu ‘alayhi wa aalihi wa sallam) adandiuza. Pitiriza kulasa mivi iwe Sa’ di! Abambo anga ndi mayi anga aperekedwe nsembe chifukwa cha iwe. Sindidaponye muvi umodzi kupatula kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adapitiriza kumupempha Allah Ta’ala kuti muvi wanga ulungame pa chandamale chake ndi kuyankha dua yanga ndikampempha.

Pomaliza, pamene mivi yonse yomwe ndinali nayo yonse inatha, Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) anatulutsa mivi ya Uta wake ndi kundipatsa muvi wakuthwa kuti nsigwiritse ntchito kuwombera panjira ya Allah Ta’ala.

Imaam Zuhri (rahimahullah) wanena kuti Sa’d (radhwiyallahu ‘anh anali ndi mivi yokwana 1000 pa nkhondo ya Uhud. (Mustadrak Haakim #4114)

Check Also

Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza …