Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 2

6. Ndi zoloredwa kuwerenga Quraan pafoni popanda wudhu. Komabe, munthu apewe kuyika dzanja lake kapena chala chake pa fonipo pomwe ndime za Qur’an zikuwonekera.

Zindikirani: Tiyenera kukumbukira kuti ngakhale kuwerenga Qur’an pa foni nkoloredwa, kuwerenga Qur’an kuchokera m’bukhu monga m’mene ilili ndi zokondedwa kwambiri chifukwa kuteroko pali kutetezedwa kwa njira yeniyeni yoiwerengera kudzera mukuwerenga motere.

Pomwe njira inayi, kuwerenga Qur’an kuchokera pa foni sikukulimbikitsidwa chifukwa foni nthawi zambiri imakhala ndi zithunzi za zinthu zamoyo ndipo machimo ambiri amachitidwa kudzera pa foni. Choncho, izi zimachititsa kuti kulemekezeka kwa Quraan Majiid kusowekere. Choncho, pofuna kukweza ma ufulu a Quraan Majiid ndikuilemekeza kwakukulu kwalimbikitsidwa kwambiri kuti Qur’an Majiid iwerengedwe mwa njira yoyambirira poyang’ana mu Quraan Majiid ndikuiwerenga m’menemo komanso kuiwerenga utapanga wudhu.

7. Khazikitsani nthawi tsiku lililonse yoti mudziwerenga Quraan Majiid.

Ibnu Umar (Radhwiyallahu anhu) akusimba kuti Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Ndithu mitima iyi imachita dzimbiri monga momwe chitsulo chimachitira dzimbiri pamene chakumana ndi madzi.” Ma Swahaabah (radhwiyallahu anhum) adafunsa kuti: “E, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam), ndi njira yanji yoyeretsera? Rasulullah (swallallahu alaihi wasallam) adayankha: “Kukumbukira imfa nthawi zambiri ndi kuwerenga Qur’an Majeed.

Check Also

Ma Sunnah Komanso Miyambo Ya Dua 2

2. Popanga dua, kwezani manja anu mofanana ndi pachifuwa chanu (i.e. molingana ndi chifuwa chanu). …