Bibi ‘Aaishah (radhwiyallahu ‘anha) akufotokoza:
Titasamuka kupita ku Madina Munawwarah, nthawi ina yake Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) sadagone usiku onse (kuopa kuti adani angamuchite chipongwe). Apa ndi pamene Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adati: “Pakadakhala munthu owopa Allah kuti andidikilire usiku uno.” Tili chikhalire choncho, tinamva kulira kwa zida. Rasulullah (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adafunsa: “Ndani amene alipo?” Munthuyo adayankha: “Sa’d bin Abi Waqqaas (radhwiyallahu ‘anhu).” Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamfunsa: “Nchiyani chakubweretsa kuno?” Sa’d (radhwiyallaahu ‘anhu) adayankha: “Ndimaopera moyo wanu Mtumiki wa Allah (swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam), choncho ndadza kudzakuyang’anirani.” Atamva izi, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adamupangira duwa ndipo kenako adagona.
M’hadith ina zikunenedwa kuti, bibi ‘Aaishah (radhwiyallahu ‘anha) adanena kuti Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adatetezedwa ndi Maswahaabah (radhwiyallahu ‘anhum) mpaka idavumbulutsidwa ndime ya Qur’an Majiid iyi:
وَاللَّهُ يَعْصِمُكَ مِنَ النَّاسِ
Ndipo Allah akuteteza ku (masautso a anthu).
Pamene ndime iyi ya Qur’an idavumbulutsidwa, Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawafotokozera maswahaba (radhwiyallahu ‘anhum) kuti: “E inu anthu pitani popeza Allah wanditsikizira kuti anditeteza! (Sunan Tirmizi #3046)