8. Umodzi mwa ma ufulu a Quraan Majiid ndi kulingalira zomwe zili mkati mwake ndi matanthauzo ake kuti uchite moyenera malamulo a Quraan Majiid. Choncho, pamodzi ndi kuwerenga Quraan Majiid, munthu ayesetsenso kuphunzira tanthauzo la ma surah osiyanasiyana a Quraan Majiid ndikofunikanso. Izi ziyenera kuchitika pansi pa Aalim oyenerera. Munthu asayambe kuphunzira yekha.
أَفَلَا يَتَدَبَّرُونَ الْقُرْآنَ أَمْ عَلَىٰ قُلُوبٍ أَقْفَالُهَا ﴿٢٤﴾
Kodi iwo sakuganizira za Qur’an, kapena m’mitima mwawo muli zotsekera?
9. Iwerengeninso Ta’awwuz (a’uuzu billah) pamene mukuyamba kuwerenga Quraan Majiid.
فَإِذَا قَرَأْتَ الْقُرْآنَ فَاسْتَعِذْ بِاللَّهِ مِنَ الشَّيْطَانِ الرَّجِيمِ ﴿٩٨﴾
Mukamawerenga Qur’an, dzitchinjirize kwa Allah kuchokea kwa Satana, wokanidwa.
10. Muiwerenge Qur’an Majiid pamene mtima wanu Ukufuna kuwerenga. Ngati mukumva kutopa ndi kuona kuti chidwi chathawa (mukuganiza zina), ndiye kuti muyenera kusiya kuwerengako ndikupitirizanso pamene maganizo anu akhanzikika.
Jundub Bin Abdillah radhwiyallahu anhu akuti Rasulullah swallallahu alaihi wasallam adanena kuti, werengani Qur’an pamene maganizo anu akhanzikika (pa qurani) ndipo ngati chidwi chanu chathawa (ndipo mwatopa) imikirani kuwerengako.