Kukhazikika kwa Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) pa Imaan

Abu “Uthmaan (rahimahullah) anasimba kuti Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adati: “Ndime iyi ya Qur’aan idavumbulutsidwa ponena za ine.

وَوَصَّيْنَا الْإِنسَانَ بِوَالِدَيْهِ حُسْنًا ۖ وَإِن جَاهَدَاكَ لِتُشْرِكَ بِي مَا لَيْسَ لَكَ بِهِ عِلْمٌ فَلَا تُطِعْهُمَا

Ife tamulamula munthu kuchitira zabwino makolo ake. Ndipo (makolo Anu osakhulupirira) Akakukakamizani kuti Mundiphatikize (ndi chipembedzo Changa) zomwe inu simukuzidziwa, Musawamvere.

Ndinali mwana omvera kwambiri kwa amayi anga. Koma nditalowa Chisilamu, adandiuza kuti: “E, iwe Sa’d! Ndi chipembedzo chanji chachilwndo chomwe wayambitsachi, usiye chipembedzo chimenechi apo ayi sindidzayankhula nawenso komanso sindidzadya kapena kumwa mpaka ndimwa lire. Ndiye iweyo udzakhala ndi mlandu wa imfa yanga popeza anthu adzakutcha kuti munthu amene anapha mayi ake.” Ndidayankha: “E, amayi anga! Musachite zimenezo chifukwa ine sindine okonzeka kusiya chipembedzo changa ichi chifukwa cha chilichonse cha padziko lapansi.”

Kenako mayi anga anakhala ndi njala kwa masiku atatu usana ndi usiku mpaka anafooka kwambiri. Nditaona ali m’mavuto otelowo ndidati kwa iwo: “E, inu mayi anga! Ndithu, ndikufuna ndikudziwitseni kuti, Mdzina la Mulungu, mukadakhala ndi miyoyo zana limodzi (100), ndipo mumwalira miyoyo yonseyo umodzi umodzi chifukwa cha kuyesayesa kwanu kundinyengerera kuti ndisiye Chisilamu sindinganasiye chipembedzo changa. Choncho, ngati mukufuna, mutha kudya ndipo ngati mutafuna khalani ndi njala” Pamene mayi a Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adawona kutsimikiza mtima kwake kosatha. Komanso kudzipereka ku Chisilamu, adazindikira kuti iye sangasiye chisilamu adamasura lumbiro lake ndikuyamba kudya. (Siyar Alaam min Nubalaa vol.3 pg. 69, Saheeh Muslim #1748)

Check Also

kuwakonda ma Answaar

Aamir (rahimahullah) mwana wa Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu), akufotokoza motere: Nthawi ina ndinati kwa bambo anga: …