Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 4

11.Werengani Quraan Majiid mwa tajwiid ndi matchulidwe olondola. Ngakhale mutamawerenga mwachangu, muyenera kuonetsetsa kuti mukuwerenga liwu lililonse momveka bwino ndi tajweed komanso katchulidwe koyenera.

وَرَتِّلِ الْقُرْآنَ تَرْتِيلًا

Ndipo werengani Qur’an momveka bwino ndi mwa tarteel (mwa pang’onopang’ono).

Zanenedwa kuti nthawi ina munthu wina adadza kwa Abdullah bin Mas’uud nati: “Ndimawerenga Surah zonse za Mufassal (kuchokera ku Surah Hujuraat mpaka kumapeto kwa Quraan Majiid) mu rakah imodzi. Atamva izi Abdullah bun Mas’uud adayankha nati: “(Kuwerenga kwako mwina) kumakhala kothamanga, monga kuwerenga ndakatulo (kuwerenga kwakoko kumakhala kofulumira komanso kopanda kutsatira malamulo a tajwiid ngati kulemba ndakatulo) Ndithu, anthu ena adzaiwerenga Qur’an Majiid Koma siidzadutsa m’mero wawo (iyo siidzakwera kupita kwa Allah ndi kulandiridwa, chifukwa choiwerenga molakwika, kapena siidzafika m’mitima mwawo ndi kupangitsa mitima yawoyo kukhudzika).

12.Ukamakamba za Qur’an, uitchule ndi dzina lolemekezeka monga kunena kuti Quraan Majiid, Quraan Kariim, Qur’an yopatulika, Qur’an Yolemekezeka, ndi zina zotero.

Check Also

Sunnah komanso miyambo yoyenera kutsatira usanayambe Kuwerenga Quraan Majiid 5

13. Iwerengere Qur’an Majeed momveka bwino. Komabe, muyenera kupewa kutengera nyimbo ndi njira za oimba, …