Ulaliki Oyamba Nzinda Wa Madinah Munawwarah Pambuyo Pa Nsamuko

Pa nthawi ya nsamuko Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) atalowa mu mzinda odalitsika wa Madina Munawwarah, anthu ambiri adali kuyembekezera mwachidwi kufika kwake.

Ena mwa iwo ndi omwe ankamukonda kwambiri Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) monga ma Ansaar (radhwiyallahu anhum) a ku Madina Munawwarah komanso Ayuda ndi ena opembedza mafano omwe ankakhala mumzindawo.

Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adapereka ulaliki wapoyera momwe adaitanira anthu ku ziphunzitso zabwino za Chisilamu. Anthu omwe sanali Asilamu anali ndi chidwi chofuna kukumana ndi munthu amene ankati ndi mneneri ndi kumva uthenga wake, choncho ambiri a iwo anabwera kudzamvera ulaliki wake.

Sayyiduna Abdullah bin Salaam radhwiyallahu anhu alowa Chisilamu

Sayyiduna Abdullah bin Salaam, yemwe adali mtsogoleri wa Chiyuda panthawiyo, akulongosora za kukumana kwake koyamba ndi Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ndi mawu awa:

“Ndidali m’gulu la anthu amene adadza kudzamuona Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam), ndipo pamene maso anga adalunjika pankhope yake yodalitsika, nthawi yomweyo ndidazindikira kuti nkhope yake siinali ya munthu wachinyengo.

Mawu oyamba amene adatuluka m’kamwa mwake modalitsika adali: “E, inu anthu! Pangani salaamu kukhala chizolowezi pakati panu. Apatseni anthu chakudya, Lumikizani ubale wanu, ndipo pempherani Swalah usiku pamene anthu ali mtulo. Mukalowa ku Jannah ndi salaam (ndi mtendere ndi chisomo chochokera kwa Allah).

Awa anali malingaliro oyamba omwe adasiyidwa mu mtima mwa olemekezeka Abdullah bin Salaam ndi ena okhudzana ndi kukongola kwa Chisilamu.

Iye adawona kuti Chisilamu ndi chipembedzo chomwe sichimangolimbikitsa chilungamo, koma chimapita patsogolo kwambiri kulimbikitsa chifundo chapamwamba ndi kukoma mtima ku zolengedwa.

Ndi chifukwa cha izi kuti pambuyo pake Abdullah bin Salaam adalowa Chisilamu.

Kukoma mtima ndi chikondi mu gawo lililonse la moyo

Tikamaganizira zochitira chifundo komanso chikondi ku zolengedwa, nthawi zambiri maganizo amathamangira ku nkhani zachifundo. Komabe, kuchitira chifundo ndi kusonyeza chikondi ku zolengedwa sikumangolekezera pa zimenezi. M’malo mwake, kukoma mtima ndi chikondi ziyenera kuonekera mbali zonse za moyo wa Msilamu. Akhale ndi mawu olimbikitsa kwa munthu oponderezedwa, kupereka uphungu kwa amene ali m’mavuto, kupereka chakudya kwa osauka, kutonthoza ofedwa, kuthandiza amene ali m’mavuto azachuma, kupereka moni kwa Msilamu otsatizana ndi kumwetulira ndi kubweretsa chisangalalo mu mtima mwake, kuyesetsa kupewa kubweretsa zowawa ndi zosokoneza kwa anthu, kaya akhale Asilamu kapena osakhala Asilamu, ndi kunyalanyaza zolakwa za anthu – zonsezi ndi zisonyezo za mzimu wachifundo ndi chikondi umene adauonetsa okondedwa wathu Mtumiki swallallahu alaihi wasallam pochitira zolengedwa m’moyo wake onse odalitsika.

Tipemphe Allah atipatse mphamvu zotsanzira Mtumiki m’mbali zonse za moyo wathu ndikutidalitsa ndi kukongola kwa Chisilamu kuti kulikonse kumene tipite, tikawalitse mfundo zoona za Sunnah ndikukhala kuitana osakhulupirira kuti alowe Chisilamu.

Check Also

Allah Ta’ala Yekha Ndi Amene Amadyetsa Zolengedwa Zonse

Tsiku lina, m’nthawi ya Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) gulu la maswahaaba a fuko la Banu …