Ulosi wa Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) okhudza Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) Kugonjetsa Qaadisiyyah

Pa mwambo wa Hajjatul Wadaa, Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adadwala ku Makka Mukarramah ndipo ankaopa kuti amwalira. Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) atabwera kudzamuona, adayamba kulira. Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamfunsa: “Bwanji ukulira?” Sa’d (Radhwiyallaahu ‘anhu) adayankha: “Ndikuopa kuti ndingamwalilire m’dziko limene ndidachita Hijrah, ndipo kudzera mu kumwalilira kuno, malipiro a Hijrah yanga sindidzawapeza.

Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kenako adapempha duwa katatu yoti Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) achire, “E, Allah! Chiritsani Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu)!”

Pambuyo pake Sa’d (Radhwiyallaahu ‘anhu) adamufunsa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti: “E, inu Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam)! Ine ndili ndi chuma chambiri, ndipo ndili ndi mwana wamkazi olemera. Ndingasiye wilo yoti chuma changa chonse chidzapelekedwe swadaqah ndikamwalira?” Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) adayankha: “Ayi.”

Kenako Sa’d (Radhwiyallaahu ‘anhu) adafunsa: “Kodi ndingapemphe magawo awiri mwa magawo atatu a chuma changa (kuti chiperekedwe sadaqah ndikamwalira)?” Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adayankha: “Ayi.”

Kenako Sa’d (Radhwiyallaahu ‘anhu) adafunsa ngati angapemphe theka la chuma chake kuti chiperekedwe sadaqa pambuyo pa imfa yake, ndipo Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adayankha motsutsa.

Pomaliza Sa’d (Radhwiyallaahu ‘anhu) adamupempha Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) kuti apemphe gawo limodzi mwa magawo atatu a chuma chake kuti chiperekedwe sadaqah pambuyo pa imfa yake. Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adayankha: “(Inde, ukhoza kupereka) gawo limodzi mwa magawo atatu, koma kusiya gawo limodzi mwa magawo atatu ndi ambiri (potsatira za ufulu wako). Ndithu, sadaqah yonse yomwe mukupereka kuchokera m’chuma chanu ndi sadaqa. Chilichonse chimene mungapereke kwa omwe amadalira inu ndi sadaqah. Zonse zomwe mkazi wanu wapeza kuchokera m’chuma chanu ndi sadaqah, ndipo kwa inu kusiya banja lanu (Mukafa) muli bwino, ndi bwino kuposa kuwasiya (umphawi) atatambasula manja awo pamaso pa anthu (opemphetsa chifukwa cha umphawi).

Pambuyo pake Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) adamulankhula Sa’d (Radhwiyallah anhu) kuti: “Ndithu iwe ukhala ndi moyo mpaka anthu ambiri apindule kudzera mwa iwe.” (Swahiyh Muslim #1628).

Ma Muhaddithiin ena amanena kuti ulosi wa Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) unkanena za Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) kuti adzagonjetsa dziko la Qaadisiyyah, kudzera mwa iye Asilamu adapindula ndipo mavuto adabwera kwa makafiri.

Check Also

kuwakonda ma Answaar

Aamir (rahimahullah) mwana wa Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu), akufotokoza motere: Nthawi ina ndinati kwa bambo anga: …