kuwakonda ma Answaar

Aamir (rahimahullah) mwana wa Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu), akufotokoza motere:

Nthawi ina ndinati kwa bambo anga: “O, bambo anga okondedwa! Ine ndikuona kuti inu mumasonyeza chikondi chowonjezera ndi ulemu kwa ma Answaar poyerekeza ndi anthu ena.”

Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adandifunsa: “E, mwana wanga! Kodi siukusangalatsidwa ndi izi?” ndinayankha, “Ayi! Sindine okondwa. Komabe, ndikusangalala kwambiri ndi njira yapadera yomwe mumawachitira (Choncho, ndikufuna kudziwa chifukwa chimene mumawasonyezera chisamaliro chapadera chimenechi).”

Kenako Sa’d (Radhwiyallaahu ‘anhu) adati: “(Chifukwa chomwe ndimasonyeza chikondi choonjezera ndi ulemu kwa iwo ndi chakuti) Ndinamumva Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) akunena kuti: Ndi nsilamu weniweni yekha amene angawakonde ma Answaar Ndipo wachinyengo yekha ndi amene angapereke mavuto kwa Answaar.” (Usdul Ghaabah 2/310)

Check Also

Ulemelero Wapamwamba wa Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) Pamaso pa Abu Bakr (Radhwiyallahu ‘anhu)

Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wa aalihi wasallam) atamwalira, ma Ansaar adasonkhana ku Saqeefah Bitti Saa’idah …