Chisilamu Chimaitanira Ku Chiyani?

M’nthawi ya Rasulullah swallallahu alaihi wasallam, anthu osiyanasiyana adayamba kulowa Chisilamu.

Uthenga wa Chisilamu ukufalikira ndikufikira madera osiyanasiyana, Aksam bin Saifi rahimahullah mtsogoleri wa banja la Tamiim, adakhala ndi chidwi chofuna kudziwa za Chisilamu. Choncho, adatumiza anthu awiri amtundu wake kuti apite ku Madina Munawwarah kuti akafufuze za Mtumiki swallallahu alaihi wasallam ndi chipembedzo chake.

Anthu awiriwa atakumana ndi Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adamufotokozera kuti atumidwa ndi mtsogoleri wawo. Kenako adamufunsa Mtumiki swallallahu alaihi wasallam “Ndiwe yani ndipo uthenga wako ndi otani?”

Mtumiki swallallahu alaihi wasallam “Ine ndine Muhammad mwana wa Abdullah, ndipo ndikuyitanira ku chisilamu.” Pambuyo pake, Mtumiki swallallahu alaihi wasallam adawerenga ndime iyi ya Quraan yolemekezeka:

إِنَّ اللَّهَ يَأْمُرُ بِالْعَدْلِ وَالْإِحْسَانِ وَإِيتَاءِ ذِي الْقُرْبَىٰ وَيَنْهَىٰ عَنِ الْفَحْشَاءِ وَالْمُنكَرِ وَالْبَغْيِ ۚ يَعِظُكُمْ لَعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ ﴿٩٠﴾

Ndithudi, Mulungu akulamula (Kuchita) chilungamo, ndikuchita Zabwino, ndi kupatsa achinansi, Ndipo akuletsa za uve ndi zoipa Ndi kupyola malire akukulangizani Kuti muzindikire ndi kukumbukira.

Nthumwi zitamva kuwerengedwa kwa aya iyi adachita chidwi ndi uthenga wake wozama komanso wokwanira, ndipo adamupempha Mtumiki Swallallahu alaihi wasallam kuti abwerezenso kuwerenga kuti aloweze. Kenako anabwerera kwa mtsogoleri wawo.

Pobwerera kwa mtsogoleri wawo, anam’fotokozera mwatsatanetsatane za mkumano wawo. Iwo adati: “Pamene tidafunsa za m’badwo wake, adangokwanira kutchula dzina lake ndi dzina la abambo ake, ndipo sadasonyeze kulemekezeka kulikonse kwa fuko lake monga momwe zimachitikira.

“Komabe, titafunsa za m’badwo wake kuchokera kwa anthu, tidapeza kuti iye akuchokera mum’badwo wapamwamba kwambiri, oyera ndi olemekezeka.” Kenako adawerenga ndime ya Qur’an patsogolo pake.

Aksam atamva ndimeyo adatsimikiza za choonadi cha Chisilamu ndipo adati: “Ndithu, Mneneri uyu akulamula ndi makhalidwe abwino ndi zochita zabwino, ndipo akuletsa khalidwe lonyozeka ndi zoipa! Ndipo musachedwe kufikira titamalizira mwa otsiriza.” Kenako adalowa Chisilamu pamodzi ndi banja lake.

Ndime yokwanira kwambiri mu Quraan Majiid

Kunena zoona, uthenga ozama omwe uli mu ndime iyi ukupezeka ndi uthenga onse ndi uzimu wa Chisilamu. Ikutsindika kufunika kokwaniritsa maufulu a Allah ndi zolengedwa, komanso kukhala ndi mtima wachikondi chokhanzikika, ukhondo ndi ulemu. Choncho, Abdullah bin Mas’uud Radhwiyallahu anhu wanena kuti aya iyi ndi ayah ya Quraan Majiid yomwe ili yokwanira kwambiri.

Pamapeto pa aya iyi nkuti Allah akuwalamula Asilamu kuti asunge zinthu zitatu pa moyo wawo ndi kusiya zinthu zitatu. Pochita zimenezi, adzapeza mzimu weniweni wa Chisilamu.

Zinthu zitatu zomwe talamulidwa kuzitsatira ndi izi:

1. Adl – Kuchita chilungamo pokwaniritsa maufulu omwe tili nawo kwa Allah ndi zolengedwa.

2. Ihsaan kupyola kufunikira kwa chilungamo ndikuchitira zabwino zolengedwa.

3. Kuwachitira zabwino abale athu monga momwe Allah wawapatsira ufulu waukulu kuposa Ife.

Zinthu zitatu zomwe talamulidwa kuzipewa ndi izi:

1. Khalidwe lopanda manyazi ndi khalidwe loipa

2. Machimo onse ndi oyipa

3. Kuponderezedwa kwa mtundu uliwonse pa lamulo a shari’ah.

Check Also

Allah Ta’ala Yekha Ndi Amene Amadyetsa Zolengedwa Zonse

Tsiku lina, m’nthawi ya Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) gulu la maswahaaba a fuko la Banu …