Magazi Oyamba Kukhetsedwa Chifukwa cha Chisilamu

Muhammad bin Ishaaq (rahimahullah) anati:

Kumayambiriro kwa Chisilamu, ma Swahaabah a Mtumiki (Swallallaahu ‘alaihi wasallam) ankaswali mobisa. Iwo ankapita kuzigwa za Makka Mukarramah kukaswali kuti Swalaah yawo ikhale yobisika kwa osakhulupirira (ndi kuti apulumuke ku mazunzo a anthu osakhulupirira).

Tsiku lina Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adali nawo pamodzi ndi gulu la ma Swahaabah ena (Radhwiyallahu ‘anhum) akuswali mu chimodzi mwa zigwa za Makkah Mukarramah, gulu la osakhulupirira lidawaona. Kenako okanirawo adayamba kuwanyoza ndi kunyoza Dini yawo mpaka kumenyana pakati pa magulu awiriwa kudayamba (ma Swahaabah Radhwiyallahu ‘anhum) ndi osakhulupirira). Pankhondoyi Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adavulazidwa ndi m’modzi mwa osakhulupirira chilonda choopsa pamutu pomenya chigaza chake ndi fupa la chibwano cha ngamira. Iyi inali nkhondo yoyamba (yomwe idachitika kuyambira kuchiyambi kwa Chisilamu momwe ma Swahaabah (Radhwiyallahu ‘anhum) adavulaza thupi makafiri ndipo idali nkhondo yomwe idakhetsedwa mwazi chifukwa cha chisilamu. (Usdul Ghaabah 2). /308)

Check Also

Ulosi wa Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) okhudza Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) Kugonjetsa Qaadisiyyah

Pa mwambo wa Hajjatul Wadaa, Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adadwala ku Makka Mukarramah ndipo ankaopa kuti …