Muvi Oyamba kulasa Mchisilamu

Olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adali m’gulu la ma Swahaabah omwe Mtumiki (swallallaahu ‘alayhi wasallam) adawatumiza m’chaka choyamba cha Hijrah kuti akalimbane ndi gulu la ma Quraishi Paulendowu, Mtumiki (sawllallahu alaihi wasallam) adamusnkha Sa’ d (radhwiyallahu anhu) kukhala mtsogoleri wa gululi, Pa ulendowu maswahaaba (radhwiyallahu ‘anhum) adapita ku Rabigh komwe adakumana ndi gulu la MaQuraishi panalibe kumenyana kulikonse pakati pa mbali ziwirizi, koma kuti mivi inalasidwa ku mbali zonse ziwiri, Munthu oyamba kuponya muvi kumbali ya Asilamu anali olemekezeka Sa’d (radhwiyallahu anhu) ndipo uwu udali muvi oyamba kulasidwa mu Chisilamu panjira ya Allah Taala.

Idali nkhondo imeneyi pamene olemekezeka Sa’d (radhwiyallah anhu) adalakatula ndakatulo iyi:

ألا هل أتى رسول الله أني    حميت صحابتي بصدور نبلي

أذود بها عدوهم ذيادا    بكل حزونة وبكل سهل

فما يعتد رام من معد    بسهم في سبيل الله قبلي

Kodi Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) wadziwitsidwa za momwe ndatetezera maswahaaba anga polasa ndikuponya zida zanga ndikuwabalitsa adani awo ndi mivi yanga kuwathamangitsa) kuchokera kumtunda uliwonse olimba ndi ofewa

Choncho kuchokera ku ana a Ma’ad palibe amene adaponya muvi m’mbuyo mwanga panjira ya Allah Ta’ala.

Check Also

Ulosi wa Rasulullah (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) okhudza Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) Kugonjetsa Qaadisiyyah

Pa mwambo wa Hajjatul Wadaa, Sa’d (Radhwiyallahu ‘anhu) adadwala ku Makka Mukarramah ndipo ankaopa kuti …