Umoyo Wa Chisilamu

Munthu akamira m’madzi n’kumavutika kuti apulumuke, angachite chilichonse kuti apulumutse moyo wake. Ngati Angakwanitse kugwira chingwe chapafupi chomwe angadzitulutse m’madzimo amachikakamira n’kumachiona ngati ndi njira yake yopulumutsira moyo.

M’dziko lino lapansi, M’silamu ngati akakumane ndi mafunde amphamvu a fitnah (mayesero) omwe akupereka chiopsezo chommiza m’machimo ndi kuononga chipembedzo chake, adzifunse kuti: “Kodi njira ya moyo ya Chisilamu ndi yotani kuti ndiitsatire mwamphamvu?

Njira yachisilamu ndikukonza ubale wako ndi Allah, Iyi ndi njira yothetsera mavuto onse, kaya okhudzana ndi chipembedzo kapena dunya.

Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) atasamuka kupita ku Madina Munawwarah, kenako m’nthawi ya Jumu’ah ya Khutba yoyamba yomwe adapereka, adalankhula kwa anthu kuti: “Amene akonze ubwenzi wake ndi Allah Ndithu, Allah Adzasamalira zinthu zake pamodzi ndi anthu ndi kuonjezera Ubale wake ndi iwo).

Kukweza ubale wa munthu ndi Allah ndiye chinsinsi chopezera chipambano padziko lapansi ndi tsiku lomaliza. Tingayerekezere ndi dzuwa limene limaunikira chilichonse padziko lapansi.

Munthu akauwalitsa moyo wake ndi chikondi cha Allah ndi kukonza ubale wake ndi Mlengi wake, ndiye kuti Allah amamudalitsa ndi thandizo lake ndi kumupatsa kupambana pa chilichonse. Ngakhale ubale wake ndi anthu umapita patsogolo ndipo anthu amayamba kumukonda.

Komabe, kuti munthu atukule ubale wake ndi Allah, nkofunikira kuti atsatire zinthu zitatu pa moyo wake.
Choyamba ndikusunga nthawi pa Swalah, chachiwiri ndi kusiya machimo, ndipo yachitatu ndi kuchitira zabwino zolengedwa, makamaka banja lako ndi achibale ako.

kulimbikira Swalaah

Swalah yafotokozedwa mu Hadith kuti ndi mzati waukulu wa Dini ya munthu. Popanda kuswali siungathe kukweza ubale wako ndi Allah ndikupeza chikondi Chake ndi chifundo Chake.

Lidali khumbo la Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) kwa amuna a mu Ummah wake kuswali Swalah za fardh ndi jamaat (gulu) mu musjid.

Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adali okonda kuswali Swalah pamodzi ndi jamaat munzikiti, kotero kuti ngakhale atadwala kwambiri asanamwalire, pamene sadathe kuyenda popanda kuthandizidwa, adayenda mothandizidwa ndi anthu awiri kupita ku mzikiti kuti akaswali.

Ponena za amuna omwe ankaswali Swalah zawo kunyumba, Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) adati: “Pakadapanda akazi ndi ana m’nyumba, ndikadaswali Swalah ndipo pambuyo pake ndidakalamula gulu la anyamata kuti liotche moto nyumba za anthu amene amaswali fardh m’nyumba zawo (popanda chowiringula).”

Mu Hadith ya olemekezeka Abdullah bin Mas’uud (radhwiyallahu anhu) zatchulidwa kuti amene akufuna kudzakumana ndi Allah pa tsiku la Qiyaamah ali Msilamu azilimbikira kuswali kasanu tsiku ndi tsiku mzikiti.

Kupewa Machimo

Kuti munthu atukule ubale wake ndi Allah kuli koyenera kwa iye kusiya machimo ndi Kudziteteza ku mayesero. Muhaddith wamkulu, ́Allaamah Yusuf Binnowri (Rahimahullah) wanena kuti: “Mu m’bado uliwonse ndi m’nyengo iliyonse, mafitnah amaonekera m’njira zosiyanasiyana. komabe mitundu iwiri ya mayesero omwe amaononga Dini, mayesero mu ilm komanso mayesero mu ntchito zabwino.

Allaamah Binnowri (Rahimahullah) adalongosola pambuyo pake kuti fitnah mu amal zimachitika pamene anthu alowa m’machimo monga maubale oletsedwa, zina, kumwa mowa ndi mankhwala osokoneza bongo, katapila, ziphuphu, kusakhala ndi manyazi, kuvina, kuyimba ndi kumvera nyimbo. Machimowa amatsogolera kuti wina alowe mu kuponderezana, kunama, kusakhulupilika, ndi zina zotero.

Zotsatira zamachimowa pamapeto pake zimakhudza Swalah, kusala, zakaat, Haji ndi ntchito zina zonse zabwino. Munthu akamachita zambiri m’machimowa ndi kumiramo, m’pamenenso dini yake imachepa mphamvu, ndipo pang’onopang’ono munthu amalephera kuchita zabwino.

Pankhani ya fitnah (mayesero) ya ilm (maphunziro a dini), izi zimachitika kudzera kuti munthu kuphunzira chipembedzo chake kuchokera ku njira zosadalirika komanso osakhala za chisilamu (monga TV, Youtube, Facebook, ndi zina zotero).

Kudzera mwa munthu ophunzira dini yake kuchokera ku magwero oipa ngati ameneŵa, mtima wake ndi malingaliro ake zidzaumbidwa moyenerera, kumpangitsa iye kukhala ndi kumvetsetsa kolakwika ndi kawonedwe ka chipembedzo. Choncho, ntchito zimene adzachite pambuyo pake zidzagwirizana ndi maganizo amene wapeza kuchokera ku magwero amenewa.

Kusonyeza Kukoma Mtima ku Zolengedwa

Kuti munthu atukule ubale wake ndi Allah nkofunika kwa iye kuchitira zabwino akapolo a Allah ndikuwakwaniritsira maufulu awo.

Kuchitira zabwino akapolo a Allah ndi njira yabwino yopezera chifundo cha Allah. Ngati munthu achitira zoipa akapolo a Allah sangapeze chikondi ndi chifundo cha Allah.

Mawu Agolide a Moulana Ilyaas Rahimahullah

Moulana Ilyaas adanena kuti pa tsiku la Qiyaamah padzakhala zinthu ziwiri zomwe zidzakondweretse Allah zomwe anthu adzapeze nazo chikhululuko.

Choyamba ndi kuonetsa ulemu ku chirichonse chokhudzana ndi dini, mwachitsanzo. Quraan Majiid, Azaan, Mizikiti, Muazzin (opanga Adhaana), ma Ulama, etc.

Chachiwiri ndi kusonyeza kukoma mtima ku zolengedwa. Zinthu ziwirizi ndizokondedwa kwambiri pa maso pa Allah ndipo zidzachititsa kuti anthu alowe ku Paradiso.

Allah wapeleka kubanja ndi achibale ako ufulu okulirapo poyerekeza ndi Asilamu wamba. kotero, munthu ali ndi udindo okulirapo ochitira achibale ake zabwino mokoma mtima ndi kukwaniritsa ufulu wawo. Kuonjezera apo, kuchitira zabwino achibale ndi njira yopezera barakah yaikulu pa moyo wa munthu.

Mtumiki (Swallallah alaihi wasallam) adanena kuti: “Amene akufuna kuti riziki lake lichulukitsidwe komanso kuti moyo wake utalikitsidwe ayenera kusunga ubale.”

Tsoka ilo, kufunikira kwakukulu kokwaniritsa ufulu wa achibale ndikusiya moyo wa Asilamu pang’onopang’ono. Palibe amene angasamalire okalamba kapena achibale amene akudwala.

Zotsatira zomvetsa chisoni n’zakuti anthu amagwa m’maganizo ndi kutaya chiyembekezo, pamene chipembedzo cha Chisilamu chimapereka chiyembekezo ndi chifundo kwa aliyense mnyengo iliyonse.

Choncho, ngati munthu akufuna kupeza chifundo chapadera cha Allah m’moyo wake, ndiye kuti chinsinsi n’chakuti apemphere Swalah yake yonse ku mzikiti pamodzi ndi jamaa, kusiya machimo onse ndikuchitira zabwino zolengedwa ndi kukwaniritsa maufulu awo.

Check Also

Allah Ta’ala Yekha Ndi Amene Amadyetsa Zolengedwa Zonse

Tsiku lina, m’nthawi ya Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) gulu la maswahaaba a fuko la Banu …