M’chaka cha 21 A.H, anthu ena aku Kufah adadza kwa Umar (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo adadandaula za Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) kuti sakumaswalitsa bwino. Nthawi imeneyo, Sa’d (radhwiyallahu anhu) adasankhidwa ndi Umar (radhwiyallahu ‘anhu) kukhala bwanamkubwa waku Kufah.
Umar (radhwiyallahu anhu) adamuitana Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) ndipo atafika adalankhula naye mwaulemu nati: “E, Abu Ishaag (ili linali dzina la mwana wake)! pemphera Swalah moyenera.
Sa’d (radhwiyallahu ‘anhu) adayankha: “Ndikulumbira mwa Allah! Ndikumawaswalitsa Swalah imene Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) anandiphunzitsa popanda kusiya gawo ina lililonse.” kenako adalongosora m’ nene Mtumiki (swallallahu alaihi wasallam) ankapemphelera ponena kuti: “Ndikamawatsogolera mu Swalah ya Esha, ndimatalikitsa rakaah ziwiri zoyamba ndikufupikitsa rakaah ziwiri zachiwiri (monga momwe Mtumiki (Swallallaahu ‘alayhi wasallam) ankaswalira” Umar (radhwiyallahu ‘anhu). Adayankha nati: “E, Abu Ishaaq! Awa ndi malingaliro enieni omwe ndidali nawo pa iwe?”
Pambuyo pake Umar (radhwiyallaahu ‘anhul) adamutumiza Sa’d (radhwiyallahu ‘anha) kuti abwerere ku Kufah pamodzi ndi anthu ochepa kuti akafufuze zomwe ankamuneneza. funsani anthu za Sa’d (radhwiyallahu anhu) Anthuwo atafunsidwa, iwo adalibe chonena za iye koma mawu omutamanda pa chilichonse chomwe ankachita.
Potsirizira pake, anafika m’chigawo cha fuko la Banu Abs osalankhula. Apa padali munthu wina dzina lake Usaamah bun Qataadah ndipo adaimirira nati: “Popeza wandifunsa za Sa’d (radhwiyallaahu ‘anhul) pali madandaulo atatu amene ndili nawo pa iye (1) samapita nawo kunkhondo, (2) Sagawa chuma mwachilungamo ndi molingana, (3) Samapereka chigamulo choyenera mzigamulo zake basi”.
Sald (Radhwiyallahu ‘anhul) atamva zabodzazi anayankha nati: “Ndikulumbira mwa Mulungu! (1) Atalikitse moyo wake, (2) Atalikitse umphawi wake, (3) ndi kumuchulukitsira pa fitnah.”
Pambuyo pake, Usaamah bin Qataadah ankati akafunsidwa ndi anthu za chikhalidwe chake, ankayankha kuti: “Ndafika pa ukalamba ndipo ndakodwa mu fitnah ndipo zonsezi zachitika chifukwa cha matemberero a Sa’d (radhwiyallaahu ‘anhul). zikundivutitsa.
M’modzi mwa osimba nkhani imeneyi, Abidul Malik, adati: “Ndidamuona [Usaamah bin Qurtaadah) pambuyo pake atakalamba ankaopseza adzakazi m’khwalala ndi kuwavutitsa.” (Saheeh Bukhari #755)