Kuyankha kuitana kwa Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) Pambuyo pa nkhondo ya Uhud.

Nthawi ina bibi Aaisha (Radhwiya Allahu ‘anha) analankhula kwa mphwake (mwana wa mlongo wake) “Urwah (rahimahullah) kuti.

“E, mwana wa mlongo wanga! Makolo ako onse (bambo ako ndi agogo ako aakazi), Zubair (Radhwiyallah “anhu) ndi Abu Bakr (radhwiyullahu ‘anhu), anali m’gulu la ma Swahaabah amene Allah Ta’ala adalankhula za iwo m’ndime yotsatirayi ponena za nkhondo ya Uhud:

الَّذِينَ اسْتَجَابُوا لِلَّهِ وَالرَّسُولِ مِن بَعْدِ مَا أَصَابَهُمُ الْقَرْحُ ۚ لِلَّذِينَ أَحْسَنُوا مِنْهُمْ وَاتَّقَوْا أَجْرٌ عَظِيمٌ ‎﴿١٧٢﴾

Iwo amene adavomera kuitana kwa Allah ndi Mtumiki ngakhale anali atavulazidwa, kwa omwe amachita ntchito zabwino mwa iwo ndi kusiya zoipa, adzapeza malipiro aakulu.

Bibi Aaishah (Radhwiya Allahu ‘anha) adanenanso kuti, “Pamene mavuto adamupeza Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) tsiku la Uhud (chifukwa cha makafiri omwe adaukira Asilamu ndi kumuvulaza Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) ndi osakhulupilira adanyamuka kumapita, Mtumiki (Swallallahu alaihi wasallam) adali ndi mantha kuti angabwerere (ndi kuyesanso kuwaukira Asilamu). Kotero Mtumiki Swallallaahu alaih wasallam adalengezetsa “ndindani yemwe adzipereke kukalimbana nawo (adani)?”

Atamva kulengezaku,mMA swahabah okwana makumi asanu ndi awiri (70) a Mtumiki (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adavomera kuitana ndikuthamangira mchigulugulu cha osakhulupirira. (Osakhulupirira adafuna kubwelera, koma atamva kuti ma Swahaahah (Radhiyallahu ‘anhum) awalondola, adasiya ganizo lawo lobwerera. M’gulu la ma Swahaabah makumi asanu ndi awiriwa munali Abu Bakr Radhwiyallahu ‘anhu) ndi Zubair. (radhwiyallahu ‘anhuu).” (Saheeh Bukhari #4272, Fat-hul Baari 7/412)

Check Also

Abu Ubaidah (Radhwiyallahu ‘anhu) aluza mano ake pa nkhondo ya Uhud

Pankhondo ya Uhud, Rasulullah (Swalla Allaahu ‘alayhi wasallam) adamenyedwa koopsa ndi adani ndipo mano awiri …